Ndipo anati kwa iye, Mbuyanga adziwa kuti ana ali anthete, ndipo nkhosa ndi zoweta ndili nazo zilinkuyamwitsa: ndipo akathamangitsa tsiku limodzi zoweta zonse zidzafa.
1 Samueli 6:10 - Buku Lopatulika Ndipo anthuwo anatero; natenga ng'ombe ziwiri zamkaka, nazimanga pagaleta, natsekera anao kwao; Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo anthuwo anatero; natenga ng'ombe ziwiri zamkaka, nazimanga pagaleta, natsekera anao kwao; Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Anthu aja adachitadi momwemo. Adatenga ng'ombe ziŵiri zamkaka nazimanga ku galeta, natsekera makonyani ake m'khola. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Anthu aja anachitadi zimenezi. Anatenga ngʼombe zamkaka ziwiri nazimanga ku galeta lija. Koma ana awo anawatsekera mʼkhola. |
Ndipo anati kwa iye, Mbuyanga adziwa kuti ana ali anthete, ndipo nkhosa ndi zoweta ndili nazo zilinkuyamwitsa: ndipo akathamangitsa tsiku limodzi zoweta zonse zidzafa.
Ndipo kunali kachisanu ndi chiwiri anati, Taonani, kwatuluka kunyanja kamtambo konga dzanja la munthu. Nati iye, Kauze Ahabu, kuti, Mangani galeta, tsikani, mvula ingakutsekerezeni.
naika likasa la Yehova pagaletapo, ndi bokosi m'mene munali mbewa zagolide ndi zifanizo za mafundo ao.
Ndipo muyang'anire, ngati likwera panjira ya malire akeake ku Betesemesi, Iye anatichitira choipa ichi chachikulu; koma likapanda kutero, tidzadziwapo kuti dzanja limene linatikantha, silili lake; langotigwera tsokali.