Ndipo tsiku ilo ndidzalanga olumpha chiundo, nadzaza nyumba ya mbuye wao ndi chiwawa ndi chinyengo.
1 Samueli 5:5 - Buku Lopatulika Chifukwa chake angakhale ansembe, angakhale ena akulowa m'nyumba ya Dagoni, palibe woponda pa chiundo cha Dagoni ku Asidodi, kufikira lero lino. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Chifukwa chake angakhale ansembe, angakhale ena akulowa m'nyumba ya Dagoni, palibe woponda pa chiundo cha Dagoni ku Asidodi, kufikira lero lino. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Chimenechi ndicho chifukwa chake chimene ansembe a Dagoni ndi anthu onse amene amaloŵa m'nyumba ya Dagoni, sapondera pa chiwundo cha nyumbayo ku Asidodi, mpaka pano. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Nʼchifukwa chake mpaka lero ansembe a Dagoni kapena wina aliyense amene amalowa mʼkachisi wa Dagoni ku Asidodi saponda pa khonde. |
Ndipo tsiku ilo ndidzalanga olumpha chiundo, nadzaza nyumba ya mbuye wao ndi chiwawa ndi chinyengo.
Ndipo kazembe wa ankhondo a Yehova anati kwa Yoswa, Vula nsapato yako pa phazi lako; pakuti malo upondapo mpopatulika. Nachita Yoswa chomwecho.
Pamene mbuye wake anauka mamawa, natsegula pakhomo pa nyumba, natuluka kunka ulendo wake, taona, mkazi wake wamng'ono, atagwa pakhomo pa nyumba ndi manja ake pachiundo.