1 Samueli 4:7 - Buku Lopatulika Ndipo Afilisti anaopa, pakuti anati, Mulungu wafika kuzithando. Ndipo iwo anati, Tsoka kwa ife! Popeza nkale lonse panalibe chinthu chotere. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo Afilisti anaopa, pakuti anati, Mulungu wafika kuzithando. Ndipo iwo anati, Tsoka kwa ife! Popeza kale lonse panalibe chinthu chotere. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Afilistiwo adachita mantha poti ankati, “Kwafika milungu kumeneko.” Ndipo adati, “Tsoka ife! Chinthu choterechi sichidachitikepo nkale lonse. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Afilisti anachita mantha pakuti iwo ankanena kuti, “Milungu yafika ku msasa. Iwo anati, ‘Tili pamavuto. Chinthu choterechi sichinachitikepo nʼkale lomwe. |
Ndipo anagulula njinga za magaleta ao, nawayendetsa molemetsa; pamenepo Aejipito anati, Tithawe pamaso pa Israele; pakuti Yehova alikuwagwirira nkhondo pa Aejipito.
Mmodzi akadapirikitsa zikwi, awiri akadathawitsa zikwi khumi, akadapanda kuwagulitsa Thanthwe lao, akadapanda kuwapereka Yehova.
Ndipo Afilistiwo pakumva kubuma pa kufuula kwao, anati, Phokoso ili la kufuula kwakukulu ku zithando za Aisraele n'lachani? Ndipo anamva kuti likasa la Yehova lidafika ku zithandozo.
Tsoka kwa ife! Adzatilanditsa ndani m'manja a milungu yamphamvu imeneyi? Milungu ija inakantha Aejipito ndi masautso onse m'chipululu ndi yomweyi.