Iwe wokhala mu Aroere, ima panjira, nusuzumire umfunse iye amene athawa, ndi mkazi amene apulumuka; nuti, Chachitidwa chiyani?
1 Samueli 4:14 - Buku Lopatulika Ndipo Eli, pakumva kubuma kwa kulira kwao, anati, Alikupokoseranji? Ndipo munthuyo anafulumira, nadza nauza Eli. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo Eli, pakumva kubuma kwa kulira kwao, anati, Alikupokoseranji? Ndipo munthuyo anafulumira, nadza nauza Eli. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Eli atamva kulirako, adafunsa kuti, “Kodi kulira kumeneku ndiye kuti kwachitika chiyani?” Tsono munthu uja adapita msanga kwa Eli, nayamba kumufotokozera. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Eli atamva kulirako anafunsa kuti, “Kodi phokosoli likutanthauza chiyani?” Tsono munthu wa fuko la Benjamini uja anapita msanga kwa Eli kukamufotokozera. |
Iwe wokhala mu Aroere, ima panjira, nusuzumire umfunse iye amene athawa, ndi mkazi amene apulumuka; nuti, Chachitidwa chiyani?
Pakufika iye, onani, Eli analikukhala pampando m'mbali mwa njira, alikuyang'anira, popeza mtima wake unanthunthumira chifukwa cha likasa la Mulungu. Pamene munthu uja anafika m'mzindamo, nanena izi, a m'mzinda monse analira.
Koma Eli anali ndi zaka makumi asanu ndi anai kudza zisanu ndi zitatu; ndipo maso ake anangokhala tong'o osapenya.