Baibulo la pa intaneti

Zotsatsa


Baibulo lonse Chipangano Chakale Chipangano Chatsopano




1 Samueli 3:7 - Buku Lopatulika

Koma Samuele sanadziwe Yehova, ndiponso mau a Yehova sanaululidwe kwa iye.

Onani mutuwo

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

Koma Samuele sanadziwe Yehova, ndiponso mau a Yehova sanaululidwe kwa iye.

Onani mutuwo

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

Pamenepo nkuti Samuele asanadziŵe Chauta, ndipo mau a Chauta nkuti asanaululidwe kwa iyeyo.

Onani mutuwo

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

Nthawiyi nʼkuti Samueli asanadziwe Yehova ndipo Mawu a Yehova nʼkuti asanawululidwe kwa iye.

Onani mutuwo



1 Samueli 3:7
5 Mawu Ofanana  

koma wakudzitamandira adzitamandire adzikweze umo, kuti ali wakuzindikira, ndi kundidziwa Ine, kuti ndine Yehova wakuchita zokoma mtima, chiweruziro, ndi chilungamo m'dziko lapansi, pakuti m'menemo ndikondwerera, ati Yehova.


ndipo anati kwa iwo, Kodi munalandira Mzimu Woyera pamene munakhulupirira? Ndipo anati, Iai, sitinamve konse kuti Mzimu Woyera waperekedwa.


Pamene ndinali mwana, ndinalankhula ngati mwana, ndinalingirira ngati mwana, ndinawerenga ngati mwana; tsopano ndakhala munthu, ndayesa chabe zachibwana.


Ndipo Yehova anabwereza kumuitana, ndi kuti, Samuele. Ndipo Samuele anauka, napita kwa Eli, nati, Ndine, pakuti mwandiitana ndithu. Koma iye anayankha, Sindinaitane, mwana wanga; kagone.


Ndipo Yehova anabwereza kumuitana Samuele nthawi yachitatu. Ndipo iye anauka napita kwa Eli, nati, Ndine, pakuti mwandiitana ndithu. Ndipo Eli anazindikira kuti ndiye Yehova amene analikuitana mwanayo.