1 Samueli 3:14 - Buku Lopatulika Chifukwa chake ndinalumbira kwa banja la Eli, kuti zoipa za banja la Elilo sizidzafafanizidwa ndi nsembe, kapena ndi zopereka, ku nthawi zonse. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Chifukwa chake ndinalumbira kwa banja la Eli, kuti zoipa za banja la Elilo sizidzafafanizidwa ndi nsembe, kapena ndi zopereka, ku nthawi zonse. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Nchifukwa chake ndikulumbira kuti mlandu wa banja la Eli sudzatha konse mpaka muyaya, ngakhale adzapereke nsembe kapena zopereka zina.” Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Nʼchifukwa chake ndinalumbira kuti, ‘Zoyipa zimene banja la Eli linandichita sizidzafafanizidwa mpaka muyaya ngakhale adzapereke nsembe kapena zopereka zina.’ ” |
Ndipo Yehova wa makamu wadzivumbulutsa yekha m'makutu mwanga, Ndithu choipa chimenechi sichidzachotsedwa pa inu kufikira inu mudzafa, ati Ambuye, Yehova wa makamu.
Ndipo Yehova anati kwa ine, Ngakhale Mose ndi Samuele akadaima pamaso panga, koma mtima wanga sukadasamalira anthu awa; muwachotse iwo pamaso panga, atuluke.
Chifukwa chake iwe usapempherere anthu awa, usawakwezere iwo mfuu kapena pemphero, usandipembedze; pakuti Ine sindidzakumvera iwe.
M'chodetsa chako muli dama, popeza ndinakuyeretsa; koma sunayeretsedwa, sudzayeretsedwanso kukuchotsera chodetsa chako, mpaka nditakwaniritsa ukali wanga pa iwe.
Motero muzipatula ana a Israele kwa kudetsedwa kwao; angafe m'kudetsedwa kwao, pamene adetsa chihema changa ali pakati pao.
Munthu akachimwira munthu mnzake oweruza adzaweruza mlandu wake; koma ngati munthu achimwira Yehova, adzampembedzera ndani? Koma ngakhale adatero, iwo aja anakhalabe osamvera mau a atate wao, chifukwa Yehova adati adzawaononga.