1 Samueli 28:2 - Buku Lopatulika Ndipo Davide anati kwa Akisi, Potero mudzadziwe chimene mnyamata wanu adzachita. Ndipo Akisi anati kwa Davide, Chifukwa chake ndidzakuika iwe ukhale wondisungira moyo wanga masiku onse. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo Davide anati kwa Akisi, Potero mudzadziwe chimene mnyamata wanu adzachita. Ndipo Akisi anati kwa Davide, Chifukwa chake ndidzakuika iwe ukhale wondisungira moyo wanga masiku onse. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Davide adayankha kuti, “Chabwino, mudzaona zimene ndichite ine mtumiki wanu.” Akisi adati, “Chabwino, ndidzakuika kuti ukhale mlonda wonditchinjiriza pa moyo wako wonse.” Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Davide anayankha kuti, “Tsono inu mudzaona zimene mtumiki wanune ndingachite.” Akisi anayankha kuti, “Chabwino ine ndidzakuyika iwe kukhala mlonda wanga moyo wako wonse.” |
Koma Hana sadakwere, chifukwa kuti anati kwa mwamuna wake Sindidzakwerako kufikira mwanayo ataleka kuyamwa, pamenepo ndidzapita naye kuti aoneke pamaso pa Yehova, ndi kukhalako chikhalire.
chifukwa chake inenso ndinampereka kwa Yehova; masiku onse a moyo wake aperekedwa kwa Yehova. Ndipo analambira Yehova pomwepo.
Ndipo Akisi anati, Waponyana nkhondo ndi yani lero? Nati Davide, Ndi a kumwera kwa Ayuda, ndi a kumwera kwa Ayerameele, ndi a kumwera kwa Akeni.
Ndipo akalonga a Afilisti ananyamuka ndi mazana ao ndi zikwi zao; ndipo Davide ndi anthu ake ananyamuka ndi a pambuyo pamodzi ndi Akisi.