Koma Abinere, mwana wa Nere, kazembe wa khamu la ankhondo a Saulo anatenga Isiboseti mwana wa Saulo, namuolotsa nanka naye ku Mahanaimu;
1 Samueli 26:14 - Buku Lopatulika ndipo Davide anaitana anthuwo, ndi Abinere mwana wa Nere, nati Suyankha kodi Abinere? Tsono Abinere anayankha, nati, Ndiwe yani amene uitana mfumuyo? Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 ndipo Davide anaitana anthuwo, ndi Abinere mwana wa Nere, nati Suyankha kodi Abinere? Tsono Abinere anayankha, nati, Ndiwe yani amene uitana mfumuyo? Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Tsono Davide adaitana gulu lankhondo ndi Abinere mwana wa Nere, naŵafunsa kuti, “Kodi sukumva iwe Abinere?” Abinere adayankha kuti, “Kodi ndiwe yani ukuitana mfumuwe?” Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Davide anayitana gulu lankhondo ndi Abineri mwana wa Neri nawafunsa kuti, “Kodi sundiyankha ine Abineri?” Abineri anayankha kuti, “Ndiwe yani amene ukuyitana mfumu?” |
Koma Abinere, mwana wa Nere, kazembe wa khamu la ankhondo a Saulo anatenga Isiboseti mwana wa Saulo, namuolotsa nanka naye ku Mahanaimu;
ndi dzina la mkazi wa Saulo ndi Ahinowamu mwana wa Ahimaazi; ndi dzina la kazembe wa khamu lankhondo lake ndiye Abinere mwana wa Nere, mbale wake wa atate wa Saulo.
Ndipo Davide anaolokera kutsidya, naima patali pamwamba paphiri; pakati pao panali danga lalikulu;
Davide nati kwa Abinere, Sindiwe mwamuna weniweni kodi? Ndani mwa Aisraele anafanafana ndi iwe? Unalekeranji tsono kudikira mbuye wako, mfumuyo? Pakuti anafika wina kudzaononga mfumu, mbuye wako.