1 Samueli 26:1 - Buku Lopatulika Ndipo Azifi anafika kwa Saulo ku Gibea, nati, Kodi Davide sali kubisala m'phiri la Hakila, kupenya kuchipululu! Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo Azifi anafika kwa Saulo ku Gibea, nati, Kodi Davide sali kubisala m'phiri la Hakila, kupenya kuchipululu! Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Tsiku lina anthu a ku Zifi adabwera kwa Saulo ku Gibea, namuuza kuti, “Davide akubisala ku phiri la Hakila limene lili kuvuma kwa Yesimoni.” Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Anthu a ku Zifi anapita kwa Sauli ku Gibeya nati, “Davide akubisala ku phiri la Hakila, limene limayangʼanana ndi Yesimoni.” |
Ndipo a ku Zifi anakwera kwa Saulo ku Gibea, nati, Davide salikubisala kwathu kodi, m'ngaka za m'nkhalango ku Horesi, m'phiri la Hakila, limene lili kumwera kwa chipululu?
Saulo namanga zithando m'phiri la Hakila kupenya kuchipululu kunjira. Koma Davide anakhala kuchipululu, naona kuti Saulo alikumfuna kuchipululu komweko.