1 Samueli 22:22 - Buku Lopatulika Ndipo Davide anati kwa Abiyatara, Tsiku lija Doegi wa ku Edomu anali kumeneko, ndinadziwiratu kuti adzauzadi Saulo; ine ndinafetsa anthu onse a nyumba ya atate wako. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo Davide anati kwa Abiyatara, Tsiku lija Doegi wa ku Edomu anali kumeneko, ndinadziwiratu kuti adzauzadi Saulo; ine ndinafetsa anthu onse a nyumba ya atate wako. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Davide adauza Abiyatara kuti “Ha! Tsiku limene lija nditaona kuti Doegi Mwedomu ali konkuja, ndidaadziŵa kuti kosapeneka konse akauza Saulo. Nchifukwa chake tsono uli pa ine mlandu wa imfa ya onse a m'banja la bambo wako. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Ndipo Davide anati kwa Abiatara, “Tsiku lija pamene Doegi Mwedomu anali kumene kuja, ine ndimadziwa kuti salephera kukamuwuza Sauli. Ine ndi amene ndaphetsa banja lonse la abambo ako. |