1 Samueli 22:12 - Buku Lopatulika Ndipo Saulo anati, Imva tsopano iwe mwana wa Ahitubi. Nayankha iye, Ndine, mbuye wanga. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo Saulo anati, Imva tsopano iwe mwana wa Ahitubi. Nayankha iye, Ndine, mbuye wanga. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Ndipo Saulo adati, “Imva tsono, iwe mwana wa Ahitubi.” Iye adayankha kuti, “Inde, mbuyanga.” Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Sauli anati, “Tsono tamvera, mwana wa Ahitubi.” Iye anayankha kuti, “Inde mbuye wanga.” |
Ndipo Mefiboseti mwana wa Yonatani, mwana wa Saulo, anafika kwa Davide, nagwa nkhope yake pansi, namlambira. Ndipo Davide anati, Mefiboseti! Nayankha iye, Ndine mnyamata wanu.
Iwo amene sanafunse za Ine andifunafuna; ndi iwo amene sanandipwaire andipeza; ndinati, Taonani Ine, taonani Ine, kwa mtundu umene sunatchule dzina langa.
Pamenepo mfumu anatuma mthenga kukaitana Ahimeleki wansembeyo, mwana wa Ahitubi, ndi banja lonse la atate wake, ansembe a ku Nobu; ndipo iwo onse anafika kwa mfumu.
Ndipo Saulo anati kwa iye, Munapangana chiwembu pa ine bwanji, iwe ndi mwana wa Yese, kuti unampatsa iye mkate, ndi lupanga, ndi kumfunsira kwa Mulungu kuti iye andiukire, kundilalira, monga lero lomwe?
Ndipo Saulo anati kwa anyamata ake akuima chomzinga, Imvani tsopano, inu a Benjamini; kodi mwana wa Yese adzakupatsani inu nonse minda, ndi minda yampesa, kodi adzakuikani mukhale atsogoleri a zikwi ndi a mazana;