Baibulo la pa intaneti

Zotsatsa


Baibulo lonse Chipangano Chakale Chipangano Chatsopano




1 Samueli 21:8 - Buku Lopatulika

Ndipo Davide ananena ndi Ahimeleki, Nanga pano m'dzanja mwanu mulibe mkondo kapena lupanga kodi? Chifukwa ine sindinatenge lupanga langa kapena zida zanga, popeza mlandu wa mfumu ukuti ndifulumire.

Onani mutuwo

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

Ndipo Davide ananena ndi Ahimeleki, Nanga pano m'dzanja mwanu mulibe mkondo kapena lupanga kodi? Chifukwa ine sindinatenge lupanga langa kapena zida zanga, popeza mlandu wa mfumu ukuti ndifulumire.

Onani mutuwo

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

Davide adafunsa Ahimeleki kuti, “Kodi kulibe mkondo kuno kapena lupanga? Paja ine sindidabwere ndi lupanga langa kapena zida zanga chifukwa ntchito ya mfumuyo inali yofulumira.”

Onani mutuwo

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

Davide anafunsa Ahimeleki kuti, “Kodi muli ndi mkondo kapena lupanga pano? Ine sindinatenge lupanga langa kapena chida china chilichonse chifukwa zimene andituma amfumu ndi zamsangamsanga.”

Onani mutuwo



1 Samueli 21:8
6 Mawu Ofanana  

Natuluka amtokoma okwera pa akavalo aliwiro achifumu; pakuti mau a mfumu anawafulumiza ndi kuwaumiriza; ndipo lamulolo linabukitsidwa m'chinyumba cha ku Susa.


Musanyamule thumba la ndalama kapena thumba la kamba, kapena nsapato; nimusalonjere munthu panjira.


Tsono munthu wina wa anyamata a Saulo anali komweko, tsiku lija, anachedwetsedwa pamaso pa Yehova; dzina lake ndiye Doegi wa ku Edomu, kapitao wa abusa a Saulo.


Nati wansembeyo, Lupanga la Goliyati Mfilisti munamuphayo m'chigwa cha Ela, onani lilipo lokulunga m'nsalu, kumbuyo kwa efodi; mukafuna kutenga limenelo, tengani; popeza pano palibe lina. Ndipo Davide anati, Palibe lina lotere longa lijalo, ndipatseni.


Ndipo Davide anati kwa Abiyatara, Tsiku lija Doegi wa ku Edomu anali kumeneko, ndinadziwiratu kuti adzauzadi Saulo; ine ndinafetsa anthu onse a nyumba ya atate wako.


Pamenepo Doegi wa ku Edomu, anaimirira ndi anyamata a Saulo, nayankha, nati, Ine ndinamuona mwana wa Yeseyo alikufika ku Nobu, kwa Ahimeleki mwana wa Ahitubi.