1 Samueli 20:7 - Buku Lopatulika Tsono akati, Chabwino; kapolo wako adzakhala ndi mtendere; koma akapsa mtima, uzindikirepo kuti anatsimikiza mtima kundichitira choipa. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Tsono akati, Chabwino; kapolo wako adzakhala ndi mtendere; koma akapsa mtima, uzindikirepo kuti anatsimikiza mtima kundichitira choipa. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Akati, ‘Chabwino’, zinthu zidzandiyendera bwino, ine kapolo wako. Koma akakhala wokwiyabe, udziŵe kuti watsimikiza mtima kuti andichita choipa. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Akanena kuti, ‘Wachita bwino,’ ndiye kuti zinthu zindiyendera bwino ine mtumiki wako. Koma ngati akapsa mtima, ndiye udziwe kuti iwo atsimikiza zondichita zoyipa. |
Ninyamuka mfumu mu mkwiyo wake ku madyerero a vinyo, nimka kumunda wa maluwa wa kuchinyumba; koma Hamani anatsalira kudzipempherera moyo kwa mkazi wamkulu Estere; popeza anapenya kuti mfumu inatsimikiza mtima kumchitira choipa.
Ndipo chinandikomera chinthu ichi; ndipo ndinatenga amuna khumi ndi awiri a inu, fuko limodzi mwamuna mmodzi;
Ndipo Saulo anamponyera mkondo kuti amgwaze; momwemo Yonatani anazindikira kuti atate wake anatsimikiza mtima kupha Davide.
Ndipo Yonatani anati, Iai ndi pang'ono ponse; ine ndikadziwa konse kuti atate wanga anatsimikiza mtima kukuchitira choipa, sindidzadziwitsa iwe kodi?
Chifukwa chake tsono mudziwe ndi kulingalira chimene mudzachita; popeza anatsimikiza mtima kuchitira choipa mbuye wathu, ndi nyumba yake yonse; popeza iye ali woipa, ndipo munthu sakhoza kulankhula naye.