Ndipo atapita masiku atatu, utsike msanga, nufike kumene unabisala tsiku la mlandu uja, nukhale pamwala wa Ezeri.
1 Samueli 20:18 - Buku Lopatulika Tsono Yonatani ananena kwa Davide, Mawa mwezi ukhala; ndipo adzakufuna, popeza udzasoweka pamalo pako. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Tsono Yonatani ananena kwa Davide, Mawa mwezi ukhala; ndipo adzakufuna, popeza udzasoweka pamalo pako. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Tsono Yonatani adatinso, “Maŵa mwezi ukhala, ndipo pa phwando adzazindikira kuti iwe palibe, popeza kuti pampando pako padzakhala popanda munthu. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Kenaka Yonatani anawuzanso Davide kuti, “Mawa ndi tsiku la chikondwerero cha mwezi watsopano. Zidzadziwika kuti iwe palibe chifukwa mpando wako udzakhala wopanda munthu. |
Ndipo atapita masiku atatu, utsike msanga, nufike kumene unabisala tsiku la mlandu uja, nukhale pamwala wa Ezeri.
Mfumu nikhala pa mpando wake, monga ankachita nthawi zina, pa mpando wa pafupi pa khoma. Ndipo Yonatani anaimirira, ndi Abinere anakhala pa mbali ya Saulo; koma Davide anasoweka pamalo pake.
Nati Davide kwa Yonatani, Onani, mawa mwezi ukhala, ndipo ine ndiyenera kupita kukadya kwa mfumu, wosatsala; koma undilole ndikabisale kuthengo, kufikira tsiku lachitatu madzulo ake.