Ndipo Abinere mwana wa Nere ndi anyamata a Isiboseti mwana wa Saulo anatuluka ku Mahanaimu kunka ku Gibiyoni.
1 Samueli 17:9 - Buku Lopatulika Akakhoza iyeyo kuponyana ndi ine ndi kundipha, tidzakhala ife akapolo anu; koma ine ndikamgonjetsa ndi kumupha, tsono mudzakhala inu akapolo athu, ndi kutitumikira ife. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Akakhoza iyeyo kuponyana ndi ine ndi kundipha, tidzakhala ife akapolo anu; koma ine ndikamlaka, ndi kumupha, tsono mudzakhala inu akapolo athu, ndi kutitumikira ife. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Ngati angathe kulimbana nane ndi kundipha, ndiye kuti Afilisti tonse tidzakhala akapolo anu. Koma ndikampambana ndi kumupha, inuyo mudzakhala akapolo athu ndi kumatigwirira ntchito. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Ngati angathe kumenyana nane ndi kundipha, ife tidzakhala akapolo anu, koma ngati ine ndimugonjetsa ndi kumupha, inu mudzakhala akapolo athu ndi kumatitumikira.” |
Ndipo Abinere mwana wa Nere ndi anyamata a Isiboseti mwana wa Saulo anatuluka ku Mahanaimu kunka ku Gibiyoni.
Pamenepo Nahasi Mwamoni anakwera, namanga Yabesi-Giliyadi zithando; ndipo anthu onse a ku Yabesi anati kwa Nahasi, Mupangane chipangano ndi ife, ndipo tidzakutumikirani inu.
Nati Mfilistiyo, Ine ndinyoza makamu a nkhondo a Israele lero; mundipatse munthu, kuti tilimbane ife awiri.