Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




1 Samueli 17:8 - Buku Lopatulika

8 Naima iye naitana makamu a nkhondo a Israele, nanena nao, Munatulukiranji kundandalitsa nkhondo yanu? Sindine Mfilisti kodi, ndi inu anyamata a Saulo? Mudzisankhire munthu, atsikire kwa ine.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

8 Naima iye naitana makamu a nkhondo a Israele, nanena nao, Munatulukiranji kundandalitsa nkhondo yanu? Sindine Mfilisti kodi, ndi inu anyamata a Saulo? Mudzisankhire munthu, atsikire kwa ine.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

8 Goliyatiyo adaimirira ndi kufuula kwa ankhondo a Aisraele kuti, “Chifukwa chiyani mukuchita kukonzekera nkhondo chotere? Ineyo ndine Mfilisti, inuyo ndinu akapolo a Saulo. Bwanji osati mungosankhula munthu pakati panupo, adze kwa ine.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

8 Goliatiyo anayimirira ndi kufuwula kwa ankhondo a Israeli, nati, “Nʼchifukwa chiyani mwakonzekera nkhondo chotere? Kodi sindine Mfilisiti ndipo inu sindinu akapolo a Sauli? Sankhani munthu kuti abwere kwa ine.

Onani mutuwo Koperani




1 Samueli 17:8
5 Mawu Ofanana  

Uriya nanena ndi Davide, Likasalo, ndi Israele, ndi Yuda, alikukhala m'misasa, ndi mbuye wanga Yowabu, ndi anyamata a mbuye wanga alikugona kuthengo, potero ndikapita ine kodi kunyumba yanga kuti ndidye, ndimwe, ndigone ndi mkazi wanga? Pali inu, pali moyo wanu, sindidzachita chinthuchi.


Nati Yowabu, Yehova aonjezere pa anthu ake monga ali kazana; koma, mbuyanga mfumu, sali onse anyamata akapolo a mbuyanga? Nanga afuniranji chinthuchi mbuyanga, adzapalamulitsa Israele bwanji?


Ndipo m'mene iye anali chilankhulire nao, onani chinakwerako chiwindacho, Mfilisti wa ku Gati, dzina lake Goliyati, wotuluka pakati pa mipambo ya Afilisti, nalankhula monga mau omwe aja; ndipo Davide anawamva.


Ndipo Davide analankhula ndi anthu akuima pafupi ndi iye, nati, Adzamchitira chiyani munthu wakupha Mfilisti uyu, ndi kuchotsa tonzo lake pakati pa Israele? Pakuti Mfilisti uyu wosadulidwa ndiye yani, kuti azinyoza makamu a Mulungu wamoyo?


Idzatenga limodzi la magawo khumi la zoweta zanu; ndipo inu mudzakhala akapolo ake.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa