Ndipo Davide anatenga mutu wa Mfilistiyo, napita nao ku Yerusalemu; koma zida zake anazisunga m'hema wake.
1 Samueli 17:57 - Buku Lopatulika Ndipo pamene Davide anabwera, atapha Mfilistiyo, Abinere anamtenga, nafika naye pamaso pa Saulo, mutu wa Mfilistiyo uli m'dzanja lake. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo pamene Davide anabwera, atapha Mfilistiyo, Abinere anamtenga, nafika naye pamaso pa Saulo, mutu wa Mfilistiyo uli m'dzanja lake. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Tsono pamene Davide ankabwererako kumene adaakapha Mfilisti kuja, Abinere adamtenga napita naye kwa Saulo, mutu wa Mfilisti uja uli m'manja mwake. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Davide atangobwerako kokapha Mfilisiti kuja, Abineri anamutenga nabwera naye kwa Sauli, mutu wa Mfilisiti uja uli mʼmanja mwake. |
Ndipo Davide anatenga mutu wa Mfilistiyo, napita nao ku Yerusalemu; koma zida zake anazisunga m'hema wake.