Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




1 Samueli 17:54 - Buku Lopatulika

54 Ndipo Davide anatenga mutu wa Mfilistiyo, napita nao ku Yerusalemu; koma zida zake anazisunga m'hema wake.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

54 Ndipo Davide anatenga mutu wa Mfilistiyo, napita nao ku Yerusalemu; koma zida zake anazisunga m'hema wake.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

54 Kenaka Davide adatenga mutu wa Mfilisti uja napita nawo ku Yerusalemu. Koma zida zokha za Mfilistiyo adaziika m'hema mwake.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

54 Pambuyo pake Davide anatenga mutu wa Mfilisitiyo napita nawo ku Yerusalemu, koma anayika zida za Mfilisitiyo mu tenti yake.

Onani mutuwo Koperani




1 Samueli 17:54
6 Mawu Ofanana  

Ndipo Mose anati kwa Aroni, Tenga mphika, nuthiremo mana odzala omeri, nuuike pamaso pa Yehova, usungikire mibadwo yanu.


Ndipo ana a Israele atathamangira Afilisti, anabwerera nafunkha za m'zithando zao.


Ndipo pamene Saulo anaona Davide alikutulukira kwa Mfilistiyo, iye anati kwa Abinere, kazembe wa khamu la nkhondo, Abinere, mnyamata uyu ndi mwana wa yani? Nati Abinere, Pali moyo wanu, mfumu, ngati ndidziwa.


Ndipo pamene Davide anabwera, atapha Mfilistiyo, Abinere anamtenga, nafika naye pamaso pa Saulo, mutu wa Mfilistiyo uli m'dzanja lake.


Nati wansembeyo, Lupanga la Goliyati Mfilisti munamuphayo m'chigwa cha Ela, onani lilipo lokulunga m'nsalu, kumbuyo kwa efodi; mukafuna kutenga limenelo, tengani; popeza pano palibe lina. Ndipo Davide anati, Palibe lina lotere longa lijalo, ndipatseni.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa