1 Samueli 17:3 - Buku Lopatulika Ndipo Afilisti anaima paphiri tsidya lija, ndi Aisraele anaima paphiri tsidya lina; ndi pakati pao panali chigwa. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo Afilisti anaima paphiri tsidya lija, ndi Aisraele anaima paphiri tsidya lina; ndi pakati pao panali chigwa. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Afilisti ndi Aisraele adaika ankhondo ao moyang'anana, ena mbali ina paphiri, ena mbali ina paphirinso, pakatipa chigwa. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Afilisti anali phiri lina ndipo Aisraeli analinso phiri lina, ndipo pakati pawo panali chigwa. |
Ndipo Saulo ndi anthu a Israele anasonkhana, namanga zithando pa chigwa cha Ela, nandandalitsa nkhondo yao kuti akaponyane ndi Afilisti.
Ndipo ku zithando za Afilisti kunatuluka chiwinda, dzina lake Goliyati wa ku Gati, kutalika kwake ndiko mikono isanu ndi umodzi ndi dzanja limodzi.