1 Samueli 17:23 - Buku Lopatulika Ndipo m'mene iye anali chilankhulire nao, onani chinakwerako chiwindacho, Mfilisti wa ku Gati, dzina lake Goliyati, wotuluka pakati pa mipambo ya Afilisti, nalankhula monga mau omwe aja; ndipo Davide anawamva. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo m'mene iye anali chilankhulire nao, onani chinakwerako chiwindacho, Mfilisti wa ku Gati, dzina lake Goliyati, wotuluka pakati pa mipambo ya Afilisti, nalankhula monga mau omwe aja; ndipo Davide anawamva. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Pamene ankalankhula ndi abale akewo, adangoona Goliyati uja akutuluka ku magulu ankhondo a Afilisti, akulankhula zonyoza zomwe zija. Davide nkumva zimenezo. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Pamene iye ankayankhula nawo anangoona Goliati wa ku Gati uja akuchoka pa mzere wa Afilisti akufuwula mawu onyoza monga mwa masiku onse, ndipo Davide ankawamva. |
Ndipo ku zithando za Afilisti kunatuluka chiwinda, dzina lake Goliyati wa ku Gati, kutalika kwake ndiko mikono isanu ndi umodzi ndi dzanja limodzi.