1 Samueli 17:11 - Buku Lopatulika Ndipo pamene Saulo ndi Aisraele onse anamva mau ao a Mfilistiyo, anadodoma, naopa kwambiri. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo pamene Saulo ndi Aisraele onse anamva mau ao a Mfilistiyo, anadodoma, naopa kwambiri. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Atamva mau a Mfilistiyo, Saulo ndi Aisraele onse adachita mantha nathyoka m'nkhongono. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Atamva mawu a Mfilisitiyo, Sauli ndi Aisraeli onse anataya mtima nachita mantha kwambiri. |
Yehova ndiye kuunika kwanga ndi chipulumutso changa; ndidzaopa yani? Yehova ndiye mphamvu ya moyo wanga; ndidzachita mantha ndi yani?
Ndipo ndi yani amene wamuopa ndi kuchita naye mantha, kuti wanama, osandikumbukira Ine, kapena kundisamalira? Kodi Ine sindinakhale chete nthawi yambiri, ndipo iwe sunandiope Ine konse?
Ndipo Yehova, Iye ndiye amene akutsogolera; Iye adzakhala ndi iwe, Iye sadzakusowa kapena kukusiya; usamachita mantha, usamatenga nkhawa.
Kodi sindinakulamulire iwe? Khala wamphamvu, nulimbike mtima, usaope, kapena kutenga nkhawa, pakuti Yehova Mulungu wako ali ndi iwe kulikonse umukako.
Ndipo Ahebri ena anaoloka Yordani nafika ku dziko la Gadi ndi Giliyadi; koma Saulo akali ku Giligala, ndipo anthu onse anamtsata ndi kunthunthumira.
Nati Mfilistiyo, Ine ndinyoza makamu a nkhondo a Israele lero; mundipatse munthu, kuti tilimbane ife awiri.
Tsono Davide anali mwana wa Mwefurati uja wa ku Betelehemu ku Yuda, dzina lake ndiye Yese; ameneyu anali nao ana aamuna asanu ndi atatu; ndipo m'masiku a Saulo munthuyo anali nkhalamba, mwa anthu.
Nasanduliza makhalidwe ake pamaso pao, nadzionetsera m'manja mwao ngati wamisala, nangolembalemba pa zitseko za chipata, nakhetsa dovu lake pa ndevu yake.
Ndipo pamene Afilisti anamva kuti Aisraele anasonkhana pamodzi ku Mizipa, mafumu a Afilisti anakwera kukayambana ndi Aisraele. Ndipo Aisraele pakumva ichi, anachita mantha ndi Afilistiwo.