1 Samueli 16:8 - Buku Lopatulika Pamenepo Yese anaitana Abinadabu nampititsa pa Samuele. Ndipo iye adati, Koma uyunso Yehova sadamsankhe. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Pamenepo Yese anaitana Abinadabu nampititsa pa Samuele. Ndipo iye adati, Koma uyunso Yehova sadamsankhe. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Tsono Yese adaitana Abinadabu namtumiza kwa Samuele. Ndipo Samuele adati, “Ameneyunso Chauta sadamsankhe.” Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Kenaka Yese anayitana Abinadabu namubweretsa pamaso pa Samueli. Koma Samueli anati, “Yehova sanamusankhenso ameneyu.” |
ndi Yese anabala mwana wake wamwamuna woyamba Eliyabu, ndi Abinadabu wachiwiri, ndi Simea wachitatu,
Ndipo ana atatu aakulu a Yese anatsata Saulo kunkhondoko; ndi maina ao a ana ake atatuwo adapita ku nkhondowo ndiwo Eliyabu woyambayo, ndi mnzake womponda pamutu pake Abinadabu, ndi wachitatu Sama.
Ndipo anthu a ku Kiriyati-Yearimu anabwera, natenga likasa la Yehova, nafika nalo m'nyumba ya Abinadabu paphiri; napatula mwana wake wamwamuna Eleazara kuti asunge likasa la Yehova.