1 Samueli 13:23 - Buku Lopatulika Ndipo a ku kaboma ka Afilisti anatuluka kunja ku mpata wa ku Mikimasi. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo a ku kaboma ka Afilisti anatuluka kunja ku mpata wa ku Mikimasi. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Tsono Afilisti adatuma kagulu kankhondo kukalonda mpata wa Mikimasi. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Tsono gulu lina lankhondo la Chifilisti linapita kukalonda mpata wa Mikimasi. |
Ndipo Afilisti anasonkhana kuti akamenyane ndi Aisraele, anali nao magaleta zikwi makumi atatu, ndi apakavalo zikwi zisanu ndi chimodzi, ndi anthu akuchuluka monga mchenga wa m'mphepete mwa nyanja. Iwowa anakwera namanga zithando ku Mikimasi kum'mawa kwa Betaveni.
Ndipo kunali tsiku lina kuti Yonatani mwana wa Saulo ananena ndi mnyamata wonyamula zida zake, Tiye tipite kunka ku kaboma ka Afilisti, tsidya lija. Koma sanauze atate wake.