1 Samueli 12:1 - Buku Lopatulika Ndipo Samuele anauza Aisraele onse, kuti, Onani ndinamvera mau anu mwa zonse munalankhula ndi ine, ndipo ndinakulongerani mfumu. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo Samuele anauza Aisraele onse, kuti, Onani ndinamvera mau anu mwa zonse munalankhula ndi ine, ndipo ndinakulongerani mfumu. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Pambuyo pake Samuele adauza Aisraele onse kuti, “Ndidamvera zonse zimene mudandiwuza, ndipo ndakupatsani mfumu kuti izikulamulirani. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Pambuyo pake Samueli anawuza Aisraeli onse kuti, “Ine ndamvera zonse zimene munandiwuza ndipo ndakupatsani mfumu kuti izikulamulirani. |
Pamenepo Samuele anatenga nsupa ya mafuta, nawatsanulira pamutu pake, nampsompsona iye, nati, Sanakudzozeni ndi Yehova kodi, Mukhale mfumu ya pa cholowa chake?
Ndipo Samuele ananena ndi anthu onse, Mumuona kodi iye amene Yehova anamsankha, kuti palibe wina wakufanana naye pakati pa anthu onse? Ndipo anthu onse anafuula, kuti, Akhale ndi moyo mfumuyo.
Chifukwa chake tsono umvere mau ao; koma uwachenjeze kolimba, ndi kuwadziwitsa makhalidwe ake a mfumu imene idzawaweruza.