Musamvere Hezekiya, pakuti mfumu ya ku Asiriya itere, Mupangane nane, tulukirani kwa ine; ndipo yense adye mphesa zake, ndi nkhuyu zake, namwe yense madzi a pa chitsime chake;
1 Samueli 11:3 - Buku Lopatulika Ndipo akulu a ku Yabesi ananena naye, Mutipatse masiku asanu ndi awiri, kuti titumize mithenga m'malire onse a Israele; ndipo pakapanda kuoneka wotipulumutsa ife, tidzatulukira kwa inu. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo akulu a ku Yabesi ananena naye, Mutipatse masiku asanu ndi awiri, kuti titumize mithenga m'malire onse a Israele; ndipo pakapanda kuoneka wotipulumutsa ife, tidzatulukira kwa inu. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Akuluakulu a ku Yabesi adamuyankha kuti, “Mutiyembekeze masiku asanu ndi aŵiri, kuti titumize mithenga ku dziko lonse la Aisraele. Tsono ngati sipaoneka wina wotipulumutsa, pamenepo tidzadzipereka kwa inu.” Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Akuluakulu a mzinda wa Yabesi anati kwa iye, “Utipatse masiku asanu ndi awiri kuti titumize uthenga mu Israeli monse. Ngati sipapezeka wodzatipulumutsa, ndiye ife tidzadzipereka kwa iwe.” |
Musamvere Hezekiya, pakuti mfumu ya ku Asiriya itere, Mupangane nane, tulukirani kwa ine; ndipo yense adye mphesa zake, ndi nkhuyu zake, namwe yense madzi a pa chitsime chake;
Chifukwa chake anthu a ku Yabesi anati, Mawa tidzatulukira kwa inu, ndipo mudzatichitira chokomera inu.