Ndipo ndidzakupatsani mtima watsopano, ndi kulonga m'kati mwanu mzimu watsopano; ndipo ndidzachotsa mtima wamwala m'thupi, ndi kukupatsani mtima wamnofu.
1 Samueli 10:9 - Buku Lopatulika Ndipo kunali, pamene iye anapotoloka kuti alekane ndi Samuele, Mulungu anampatsa mtima wina watsopano; ndipo zizindikiro zija zonse zinachitika tsiku lija. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo kunali, pamene iye anapotoloka kuti alekane ndi Samuele, Mulungu anampatsa mtima wina watsopano; ndipo zizindikiro zija zonse zinachitika tsiku lija. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Pamene Saulo adatembenuka kuti asiyane ndi Samuele, mtima wake Mulungu adausandutsa winawina. Ndipo zizindikiro zonse zija zidachitikadi tsiku limenelo. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Sauli akutembenuka kusiyana ndi Samueli, Mulungu anasintha mtima wa Sauli, ndipo zinthu zonsezi zinakwaniritsidwa tsiku lomwelo. |
Ndipo ndidzakupatsani mtima watsopano, ndi kulonga m'kati mwanu mzimu watsopano; ndipo ndidzachotsa mtima wamwala m'thupi, ndi kukupatsani mtima wamnofu.
Ndipo ophunzira anatuluka, nafika m'mzinda, napeza monga anati kwa iwo; ndipo anakonza Paska.
Pamenepo mthenga wa Yehova anatambasula nsonga ya ndodo inali m'dzanja lake, nakhudza nyamayi ndi mikate yopanda chotupitsa; ndipo unatuluka moto m'thanthwe nunyeketsa nyama ndi mikate yopanda chotupitsa; ndi mthenga wa Yehova anakanganuka pamaso pake.
nudzamva zonena iwo; utatero manja ako adzalimbikitsidwa kutsikira kumisasa. Pamenepo anatsikira ndi Pura mnyamata wake ku chilekezero cha anthu azida a m'misasa.
Pamenepo Samuele anatenga nyanga ya mafuta, namdzoza pakati pa abale ake; ndipo mzimu wa Yehova unalimbika pa Davide kuyambira tsiku lomweli. Ndipo Samuele ananyamuka, nanka ku Rama.
Ndipo ndidzadziukitsira wansembe wokhulupirika, amene adzachita monga chimene chili mumtima mwanga ndi m'chifuniro changa; ndipo ndidzammangira nyumba yokhazikika, ndipo iyeyu adzayenda pamaso pa wodzozedwa wanga masiku onse.