Baibulo la pa intaneti

Zotsatsa


Baibulo lonse Chipangano Chakale Chipangano Chatsopano




1 Samueli 10:4 - Buku Lopatulika

Iwowa adzakupatsani moni, ndi kukupatsani mikate iwiri; imeneyi mudzailandira m'manja mwao.

Onani mutuwo

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

Iwowa adzakupatsani moni, ndi kukupatsani mikate iwiri; imeneyi mudzailandira m'manja mwao.

Onani mutuwo

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

Atakupatsa moni, akuninkhako mitanda iŵiri ya buledi, iwe uilandire.

Onani mutuwo

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

Adzakupatsa moni ndi kukupatsa malofu awiri a buledi. Iwe udzalandire bulediyo.

Onani mutuwo



1 Samueli 10:4
4 Mawu Ofanana  

Napatuka iwo kunkako, nafika kunyumba ya mnyamata Mleviyo, ndiyo nyumba ya Mika, namfunsa ngati ali bwanji.


Mukapitirira pamenepo tsono ndi kufika ku mtengo wathundu wa ku Tabori, kumeneko adzakomana nanu anthu atatu akukwera kwa Mulungu ku Betele, wina wonyamula anaambuzi atatu, wina mikate itatu, wina thumba la vinyo.


Ndipo m'tsogolo mwake mudzafika kuphiri la Mulungu, kumene kuli kaboma ka Afilisti; ndipo kudzali kuti pakufika inu kumzindako mudzakomana ndi gulu la aneneri, alikutsika kumsanje ndi chisakasa, ndi lingaka, ndi chitoliro, ndi zeze, pamaso pao; iwo adzanenera;


Ndipo Yese anatenga bulu namsenza mkate, ndi thumba la vinyo, ndi mwanawambuzi, nazitumiza kwa Saulo ndi Davide mwana wake.