Pamenepo analowa, naima kwa mbuye wake. Ndipo Elisa ananena naye, Ufuma kuti Gehazi? Nati, Ngati mnyamata wanu wayenda konse?
1 Samueli 10:14 - Buku Lopatulika Ndipo mbale wa atate wake wa Saulo ananena kwa iye ndi mnyamata wake, Munanka kuti? Ndipo iye anati, Kukafuna abuluwo; ndipo pakuona kuti sitinawapeze, tinadza kwa Samuele. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo mbale wa atate wake wa Saulo ananena kwa iye ndi mnyamata wake, Munanka kuti? Ndipo iye anati, Kukafuna abuluwo; ndipo pakuona kuti sitinawapeza, tinadza kwa Samuele. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Mbale wa bambo wake wa Saulo ataona Sauloyo ndi mnyamata uja, adaŵafunsa kuti, “Mudaapita kuti?” Saulo adayankha kuti, “Tidaakafunafuna abulu. Titaona kuti sakupezeka, tidaapita kwa Samuele.” Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Tsono amalume ake a Sauli anamufunsa ndi mnyamata wake kuti, “Munapita kuti?” Iye anayakha, “Timakafunafuna abulu koma titaona kuti sakupezeka, tinapita kwa Samueli.” |
Pamenepo analowa, naima kwa mbuye wake. Ndipo Elisa ananena naye, Ufuma kuti Gehazi? Nati, Ngati mnyamata wanu wayenda konse?
ndi dzina la mkazi wa Saulo ndi Ahinowamu mwana wa Ahimaazi; ndi dzina la kazembe wa khamu lankhondo lake ndiye Abinere mwana wa Nere, mbale wake wa atate wa Saulo.