Ndipo ana ako onse adzaphunzitsidwa ndi Yehova; ndipo mtendere wa ana ako udzakhala waukulu.
1 Samueli 10:12 - Buku Lopatulika Ndipo munthu wina wa komweko anayankha nati, Ndipo atate wao ndiye yani? Chifukwa chake mauwa anakhala ngati mwambi, Kodi Saulonso ali mwa aneneri? Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo munthu wina wa komweko anayankha nati, Ndipo atate wao ndiye yani? Chifukwa chake mauwa anakhala ngati mwambi, Kodi Saulonso ali mwa aneneri? Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Munthu wina wakomweko adayankhako nati, “Nanga enaŵa ndiye abambo ao ndani?” Nchifukwa chake padayambika chisudzo chakuti, “Kani Saulonso ali m'gulu la aneneri?” Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Munthu wina wa kumeneko anayankha kuti, “Nanga enawa abambo awo ndani?” Kotero kunayambika mwambi wakuti, “Kodi Saulinso ali mʼgulu la aneneri?” |
Ndipo ana ako onse adzaphunzitsidwa ndi Yehova; ndipo mtendere wa ana ako udzakhala waukulu.
Chalembedwa mwa aneneri, Ndipo adzakhala onse ophunzitsidwa ndi Mulungu. Yense amene adamva kwa Atate, naphunzira, adza kwa Ine.
Pamenepo Yesu anayankha iwo, nati, Chiphunzitso changa sichili changa, koma cha Iye amene anandituma Ine.
Mphatso iliyonse yabwino, ndi chininkho chilichonse changwiro zichokera Kumwamba, zotsika kwa Atate wa mauniko, amene alibe chisanduliko, kapena mthunzi wa chitembenukiro.
Ndipo anapita komweko ku Nayoti mu Rama; ndi mzimu wa Mulungu unamgwera iyenso; ndipo anapitirira, nanenera, mpaka anafika ku Nayoti mu Rama.
Ndiponso anavula zovala zake, naneneranso pamaso pa Samuele, nagona wamaliseche usana womwe wonse, ndi usiku womwe wonse. Chifukwa chake amati, Kodi Saulonso ali pakati pa aneneri?