Eksodo 3:8 - Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero8 Choncho ndabwera kuti ndiwapulumutse mʼdzanja la Aigupto, kuwatulutsa mʼdzikolo ndi kukawalowetsa mʼdziko labwino ndi lalikulu, dziko loyenda mkaka ndi uchi, kwawo kwa Akanaani, Ahiti, Aamori, Aperezi, Ahivi ndi Ayebusi. Onani mutuwoBuku Lopatulika8 ndipo ndatsikira kuwalanditsa m'manja a anthu a Ejipito, ndi kuwatulutsa m'dziko lija akwere nalowe m'dziko labwino ndi lalikulu, m'dziko moyenda mkaka ndi uchi ngati madzi; ku malo a Akanani, ndi Ahiti, ndi Aamori, ndi Aperizi, ndi Ahivi, ndi Ayebusi. Onani mutuwoChichewa Buku Lopatulika Bible 20148 ndipo ndatsikira kuwalanditsa m'manja a anthu a Ejipito, ndi kuwatulutsa m'dziko lija akwere nalowe m'dziko labwino ndi lalikulu, m'dziko moyenda mkaka ndi uchi ngati madzi; ku malo a Akanani, ndi Ahiti, ndi Aamori, ndi Aperizi, ndi Ahivi, ndi Ayebusi. Onani mutuwoBuku Loyera Catholic Edition - Chichewa8 Ndabwera kuti ndiŵapulumutse kwa Aejipito ndi kuŵatulutsa m'dziko limenelo, kuti ndikaŵaloŵetse m'dziko lalikulu lachonde. Dziko limenelo ndi lamwanaalirenji. Amene akukhala m'dziko limenelo ndi Akanani, Ahiti, Aamori, Aperizi, Ahivi ndi Ayebusi. Onani mutuwo |
Aisraeli anakhala akuyenda mʼchipululu kwa zaka makumi anayi mpaka amuna onse amene potuluka mʼdziko la Igupto anali a msinkhu woyenera kupita ku nkhondo anamwalira. Iwo anafa chifukwa sanamvere mawu a Yehova. Yehova anawalumbirira kuti sadzalowa konse mʼdziko loyenda mkaka ndi uchi limene analonjeza kwa makolo awo kuti adzatipatsa.