Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Eksodo 22:3 - Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

3 Koma akayipha dzuwa litatuluka, woyiphayo ali ndi mlandu wakupha. “Mbala iyenera kubweza ndithu koma ngati ilibe kalikonse igulitsidwe, kulipira zomwe yabazo.

Onani mutuwo Koperani

Buku Lopatulika

3 Litamtulukira dzuwa, pali chamwazi; wakubayo azilipa ndithu; ngati alibe kanthu, amgulitse pa umbala wake.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

3 Litamtulukira dzuwa, pali chamwazi; wakubayo azilipa ndithu; ngati alibe kanthu, amgulitse pa umbala wake.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

3 Koma ikaphedwa dzuŵa litatuluka, apo padzakhala kulipsira magazi. Pajatu wakuba aliyense ayenera kulipira ndithu. Ngati mbala igwidwa, ndipo ilephera kulipira mlandu, aigulitse chifukwa cha kubako.

Onani mutuwo Koperani




Eksodo 22:3
9 Mawu Ofanana  

Iye anati, “Chabwino, tsono zikhale monga mwaneneramu. Komatu aliyense amene angapezeke nacho chikhocho adzakhala kapolo wanga, ndipo ena nonsenu muzipita mwaufulu.”


“Mukagula kapolo wa Chihebri, azikugwirirani ntchito zaka zisanu ndi chimodzi. Koma mʼchaka cha chisanu ndi chiwiri muzimumasula, ndipo asalipire kanthu.


mwini dzenjelo amulipire mwini chiweto chakufacho koma iye atenge chiwetocho.


“Ngati mbala ipezeka ikuthyola nyumba ndipo imenyedwa nʼkufa, amene wapha mbalayo sanalakwe.


Ayankhuleni moleza mtima anthu a ku Yerusalemu ndipo muwawuzitse kuti nthawi ya ukapolo wawo yatha, tchimo lawo lakhululukidwa. Ndawalanga mokwanira chifukwa cha machimo awo onse.


Yehova akuti, “Kalata imene ndinasudzulira amayi anu ili kuti? Kapena mwa anthu amene ndili nawo ngongole, ndinakugulitsani kwa ati? Inu munagulitsidwa ku ukapolo chifukwa cha machimo anu; amayi anu anachotsedwa chifukwa cha kulakwa kwanu.


Popeza sakanatha kubweza, bwanayo analamula kuti iye, mkazi wake, ana ake ndi zonse anali nazo zigulitsidwe kuti zibweze ngongoleyo.


Tsono Yehova anapsera mtima Aisraeli ndipo anawapereka mʼmanja mwa Afilisti ndi Aamoni.


Yehova anapsera mtima Aisraeli ndipo anawapereka mʼmanja mwa anthu ofunkha amene ankasakaza zinthu zawo. Ndipo analola kuti adani awo owazungulira amene sanathenso kulimbana nawo, awagonjetse.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa