Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Eksodo 15:3 - Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

3 Yehova ndi wankhondo; Yehova ndilo dzina lake.

Onani mutuwo Koperani

Buku Lopatulika

3 Yehova ndiye wankhondo; dzina lake ndiye Yehova.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

3 Yehova ndiye wankhondo; dzina lake ndiye Yehova.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

3 Chauta ndi wankhondo, Chauta ndilo dzina lake.

Onani mutuwo Koperani




Eksodo 15:3
14 Mawu Ofanana  

Kodi Mfumu yaulemereroyo ndani? Yehova Wamphamvuzonse, Yehova ndiye wamphamvu pa nkhondo.


Mangirirani lupanga lanu mʼchiwuno mwanu, inu munthu wamphamvu; mudziveke nokha ndi ulemerero ndi ukulu wanu.


Adziwe kuti Inu amene dzina lanu ndi Yehova, ndinu nokha Wammwambamwamba pa dziko lonse lapansi.


Yehova adzakumenyerani nkhondo. Inu mungokhala chete.”


Yehova anamanga matayala a magaleta kotero kuti ankavutika kuyenda. Ndipo Aigupto anati, “Tiyeni tiwathawe Aisraeli! Yehova akuwamenyera nkhondo kulimbana nafe.”


Mose anati kwa Mulungu, “Ngati ndipita kwa Aisraeli ndi kukawawuza kuti, ‘Mulungu wa makolo anu wandituma kwa inu,’ ndipo iwo nʼkukandifunsa kuti ‘Dzina lake ndi ndani?’ Tsono ine ndikawawuze chiyani?”


Mulungu anati kwa Mose, “NDINE AMENE NDILI. Izi ndi zimene ukanene kwa Aisraeli: ‘NDINE wandituma kwa inu.’ ”


Mulungu anatinso kwa Mose, “Ukanene kwa Aisraeli kuti ‘Yehova, Mulungu wa makolo anu, Mulungu wa Abrahamu, Mulungu wa Isake, ndi Mulungu wa Yakobo, wandituma kwa inu.’ Ili ndilo dzina langa mpaka muyaya, ndipo mibado ya mʼtsogolomo izidzanditchula ndi dzina limeneli.


Yehova adzapita ku nkhondo ngati munthu wamphamvu, adzawutsa ukali wake ngati munthu wankhondo; akukuwa ndiponso akufuwula mfuwu wankhondo ndipo adzagonjetsa adani ake.


“Ine ndine Yehova: dzina langa ndi limenelo! Sindidzapereka ulemerero wanga kwa wina aliyense kapena matamando anga kwa mafano.


“Yehova amene analenga dziko lapansi, kuliwumba ndi kulikhazikitsa; amene dzina lake ndi Yehova, akuti,


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa