Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Eksodo 11:3 - Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

3 Tsono Yehova anachititsa Aigupto kuti akomere mtima Aisraeli. Komanso Mose anali wotchuka kwambiri mʼdziko la Igupto, pamaso pa nduna za Farao ndi anthu onse.

Onani mutuwo Koperani

Buku Lopatulika

3 Ndipo Yehova anawapatsa anthu chisomo pamaso pa Aejipito. Munthuyo Mose ndiyenso wamkulu ndithu m'dziko la Ejipito, pamaso pa anyamata a Farao, ndi pamaso pa anthu.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

3 Ndipo Yehova anawapatsa anthu chisomo pamaso pa Aejipito. Munthuyo Mose ndiyenso wamkulu ndithu m'dziko la Ejipito, pamaso pa anyamata a Farao, ndi pamaso pa anthu.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

3 Ndipo Chauta adafeŵetsa Aejipito kuti akomere Aisraele mtima. Chinanso nkuti Mose anali wotchuka kwambiri m'dziko la Ejipito, pamaso pa nduna za Farao ndiponso pamaso pa anthu onse.

Onani mutuwo Koperani




Eksodo 11:3
14 Mawu Ofanana  

“Ndidzakusandutsa kholo la mtundu waukulu wa anthu ndipo ndidzakudalitsa; ndi kukusandutsa wotchuka kotero kuti udzakhala dalitso kwa anthu ambiri.


koma Yehova anali naye, ndipo anamuonetsa kukoma mtima kwake, kotero kuti woyangʼanira ndende anakondwera ndi Yosefe.


Ineyo ndinali nawe kulikonse kumene unkapita, ndipo ndachotsa adani ako onse pamaso pako. Tsopano ndidzakuza dzina lako kuti likhale mʼgulu la mayina a anthu otchuka kwambiri pa dziko lapansi.


Pajatu Mordekai anali munthu wamkulu mʼnyumba ya ufumu. Mbiri yake inafalikira zigawo zonse, ndipo mphamvu zake zinakulirakulirabe.


Iye anachititsa kuti amene anawagwira iwo ukapolo awamvere chisoni.


Aisraeli anachita monga anawawuzira Mose kuti apemphe kwa Aigupto zozikongoletsera zasiliva ndi zagolide ndi zovala.


Yehova anafewetsa mtima Aigupto kuti akomere mtima Aisraeliwo ndipo anawapatsa zimene anawapempha. Motero Aisraeli anawalanda zinthu Aigupto.


“Ndipo ine ndidzafewetsa mtima wa Aigupto pa anthu anga, kotero kuti mukadzatuluka simudzapita wopanda kanthu.


Ana aja amene anakuzunzani adzabwera ndipo adzakugwadirani; onse amene anakunyozani adzagwada pansi pa mapazi anu. Ndipo adzakutchani kuti Mzinda wa Yehova; Ziyoni mzinda wa Woyerayo wa Israeli.


Mose anaphunzira nzeru zonse za Aigupto, ndipo anali wamphamvu mʼmawu ndi ntchito zake.


Kuyambira nthawi imeneyi, mu Israeli simunakhalepo mneneri wina aliyense wofanana ndi Mose, amene Yehova amayankhula naye maso ndi maso.


Amene anachita zizindikiro zozizwitsa zonsezi ndi zozizwitsa zimene Yehova anamutuma kuti achite mu Igupto, kwa Farao ndi kwa nduna zake zonse ndiponso mʼdziko lake lonse.


Zimene Yehova anachita tsiku limeneli zinapatsa anthu mtima wolemekeza Yoswa. Ndipo anamulemekeza masiku onse a moyo wake, monga momwe analemekezera Mose.


Amene ndi mpingo wa Satana, amene amadzitcha kuti ndi Ayuda pamene sali choncho, koma ndi onama, ndidzawabweretsa kwa inu ndi kuwagwetsa pansi pa mapazi anu kuti adzazindikire kuti ndimakukondani.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa