Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Eksodo 11:2 - Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

2 Awuze anthu kuti mwamuna aliyense ndi mkazi aliyense apemphe kwa mnansi wake ziwiya zasiliva ndi golide.”

Onani mutuwo Koperani

Buku Lopatulika

2 Lankhula tsopano m'makutu a anthu, kuti mwamuna yense apemphe kwa mnzake, ndi mkazi yense kwa mnzake, zokometsera zasiliva ndi zagolide.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

2 Lankhula tsopano m'makutu a anthu, kuti mwamuna yense apemphe kwa mnzake, ndi mkazi yense kwa mnzake, zokometsera zasiliva ndi zagolide.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

2 Tsopano lankhula ndi anthu, ndipo uuze mwamuna aliyense ndi mkazi aliyense, kuti apemphe zodzikongoletsera zasiliva ndi zagolide kwa Mwejipito aliyense woyandikana naye.”

Onani mutuwo Koperani




Eksodo 11:2
16 Mawu Ofanana  

Kenaka wantchitoyo anatulutsa ziwiya zagolide ndi zasiliva ndi zovala nazipereka kwa Rebeka. Anaperekanso mphatso zina za mtengowapatali kwa mlongo wake ndi amayi ake a Rebeka.


Motero Mulungu walanda abambo anu ziweto zawo ndi kundipatsa.


Yehova anatulutsa Israeli, atatenga siliva ndi golide wambiri, ndipo pakati pa mafuko awo palibe mmodzi amene anafowoka.


Dziko lapansi ndi la Yehova ndi zonse zimene zili mʼmenemo, dziko ndi onse amene amakhala mʼmenemo;


“Ndipo ine ndidzafewetsa mtima wa Aigupto pa anthu anga, kotero kuti mukadzatuluka simudzapita wopanda kanthu.


Mkazi aliyense adzapemphe Mwigupto woyandikana naye ndiponso mkazi amene akukhala mʼnyumba yake, kuti amupatse ziwiya za siliva ndi golide ndiponso zovala zimene mudzaveka ana anu aamuna ndi aakazi. Ndipo potero mudzawalanda zonse Aiguptowo.”


Choncho ine ndinawawuza kuti, ‘Aliyense amene ali ndi zokometsera zagolide azivule.’ Choncho iwo anandipatsa golide, ndipo ndinamuponya pa moto ndi kupanga fano la mwana wangʼombeyu.”


Onse amene anali ndi mtima wofuna, amuna ndi amayi omwe anabwera kudzapereka zodzikometsera zagolide za mtundu uliwonse: zomangira zovala, ndolo, mphete ndi zokometsera. Onse anapereka golide wawo monga nsembe yoweyula pamaso pa Yehova.


Munthu wabwino amasiyira zidzukulu zake cholowa, koma chuma cha munthu wochimwa amachilandira ndi olungama.


‘Siliva yense ndi wanga, golide yense ndi wanganso,’ akutero Yehova Wamphamvuzonse.


Kodi ndilibe ufulu wochita zimene ndikufuna ndi ndalama zanga? Kapena ukuyipidwa chifukwa ndine wopereka mowolowamanja?’


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa