Danieli 7:4 - Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero4 “Choyamba chinali ngati mkango, ndipo chinali ndi mapiko ngati a chiwombankhanga. Ndinayangʼanitsitsa, kenaka mapiko ake anakhadzuka ndipo chinanyamulidwa ndi kuyimirira ndi miyendo yake iwiri ngati munthu, ndipo anachipatsa mtima wa munthu. Onani mutuwoBuku Lopatulika4 Choyamba chinanga mkango, chinali nao mapiko a chiombankhanga, ndinapenyera mpaka nthenga zake zinathothoka, ndipo chinakwezeka kudziko, ndi kuimitsidwa ndi mapazi awiri ngati munthu, ndipo chinapatsidwa mtima wa munthu. Onani mutuwoChichewa Buku Lopatulika Bible 20144 Choyamba chinanga mkango, chinali nao mapiko a chiombankhanga, ndinapenyera mpaka nthenga zake zinathothoka, nichinakwezeka kudziko, ndi kuimitsidwa ndi mapazi awiri ngati munthu, nichinapatsidwa mtima wa munthu. Onani mutuwo |
“Monga mkango wotuluka ku nkhalango za ku Yorodani kupita ku malo a msipu wobiriwira, Ine ndidzapirikitsa anthu a ku Edomu mwadzidzidzi kuchoka mʼdziko lawo. Pambuyo pake ndidzawayikira owalamulira amene ndamufuna Ine. Kodi ndani wofanana nane, ndipo angatsutsane nane ndani? Ndipo ndi mʼbusa uti amene angalimbane nane?”