Uriya anayankha Davide kuti, “Bokosi la Chipangano ndi Israeli ndiponso Yuda akukhala mʼmatenti, ndipo mbuye wanga Yowabu ndi ankhondo anu mbuye wanga amanga misasa pa mtetete. Ine ndingapite bwanji ku nyumba yanga kukadya ndi kumwa ndiponso kugona ndi mkazi wanga? Pali inu wamoyo, ine sindidzachita chinthu chimenechi.”
Tsono Hiramu mfumu ya Turo inatumiza amithenga ake kwa Davide, pamodzi ndi mitengo ya mkungudza ndi amisiri a matabwa ndi amisiri a miyala, ndipo anamumangira Davide nyumba yaufumu.
Hiramu mfumu ya ku Turo inatumiza amithenga kwa Davide pamodzi ndi mitengo ya mkungudza ndiponso amisiri a miyala ndi amisiri a matabwa kuti adzamumangire nyumba yaufumu.
Tsono zonse zimene mfumu Davide anachita, kuyambira pachiyambi mpaka pa mapeto, zalembedwa mʼbuku la mneneri Samueli, mʼbuku la mneneri Natani ndi mʼbuku la mneneri Gadi,
Davide anabweretsa Bokosi la Mulungu kuchokera ku Kiriyati Yearimu, ndi kulikhazika kumalo kumene analikonzera popeza analimangira tenti mu Yerusalemu.
Iye anayika Alevi mʼNyumba ya Yehova ali ndi ziwaya za malipenga, azeze ndi apangwe potsata lamulo la Davide, Gadi mlosi wa mfumu ndi mneneri Natani. Pakuti Yehova ndiye analamula zimenezi kudzera mwa aneneri.
Tsono ntchito zina zonse za Solomoni, kuyambira pachiyambi mpaka kumaliza, kodi sizinalembedwa mʼbuku la mbiri la mneneri Natani, ndi mʼbuku la uneneri wa Ahiya wa ku Silo ndi mʼbuku la masomphenya a mlosi Ido, lokamba za Yeroboamu mwana wa Nebati?