Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Zekariya 8:10 - Buku Lopatulika

10 Pakuti asanafike masiku aja, panalibe kulipidwira munthu, kapena kulipidwira nyama, ndipo analibe mtendere iye wakutuluka, kapena wakulowa, chifukwa cha wosautsa; pakuti ndinatumiza munthu yense atsutsane naye mnzake.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

10 Pakuti asanafike masiku aja, panalibe kulipidwira munthu, kapena kulipidwira nyama, ndipo analibe mtendere iye wakutuluka, kapena wakulowa, chifukwa cha wosautsa; pakuti ndinatumiza munthu yense atsutsane naye mnzake.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

10 Mpaka nthaŵi imeneyo panalibe wina wolandirapo malipiro pa ntchito kapena wopindulapo pa zoŵeta. Panalibe munthu amene ankadziyendera mwamtendere, chifukwa cha adani, popeza kuti anthu onse ndidaaŵayambanitsa.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

10 Mpaka nthawi imeneyi panalibe munthu wolandira malipiro pa ntchito kapena ndalama zolipirira nyama zogwira ntchito. Panalibe munthu amene ankadzigwirira ntchito mwamtendere chifukwa choopa adani ake, pakuti Ine ndinkawayambanitsa.

Onani mutuwo Koperani




Zekariya 8:10
11 Mawu Ofanana  

Ndipo ndidzapikisanitsa Aejipito; ndipo adzamenyana wina ndi mbale wake, ndi wina ndi mnansi wake; mzinda kumenyana ndi mzinda, ndi ufumu kumenyana ndi ufumu.


Taonani, ndidzaitana akugwira nsomba ambiri, ati Yehova, ndipo adzawagwira iwo, pambuyo pake ndidzaitana osaka nyama ambiri, ndipo adzasaka iwo m'mapiri onse, ndi pa zitunda zonse, ndiponso m'mapanga a m'matanthwe.


Kodi adzaomba lipenga m'mzinda osanjenjemera anthu? Kodi choipa chidzagwera mzinda osachichita Yehova?


Angakhale alowa ndende pamaso pa adani ao, kumeneko ndidzalamulira lupanga, ndipo lidzawapha; ndipo ndidzayang'anitsa maso anga kwa iwowa, kuwachitira choipa, si chokoma ai.


Ndipo tsono, samalirani, kuyambira lero ndi m'tsogolomo, kuti, kusanaikidwe mwala pamwala mu Kachisi wa Yehova,


Posamveka phokoso la amauta potunga madzi, pomwepo adzafotokozera zolungama anazichita Yehova, zolungama anazichita m'madera ake, mu Israele. Pamenepo anthu a Yehova anatsikira kuzipata.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa