Zekariya 7:7 - Buku Lopatulika7 Si ndiwo mau Yehova anawalalikira mwa aneneri oyamba aja, muja Yerusalemu anali nao okhalamo, ndi wokhazikika; ndi m'mizinda mwake pozungulira pake, ndi m'dziko la kumwera, ndi m'chidikha munali anthu okhalamo? Onani mutuwoChichewa Buku Lopatulika Bible 20147 Si ndiwo mau Yehova anawalalikira mwa aneneri oyamba aja, muja Yerusalemu anali nao okhalamo, ndi wokhazikika; ndi m'midzi mwake pozungulira pake, ndi m'dziko la kumwera, ndi m'chidikha munali anthu okhalamo? Onani mutuwoBuku Loyera Catholic Edition - Chichewa7 Pajatu nzimenezi zija ankanena Chautazi kudzera mwa aneneri akale, pamene munali modzaza ndi anthu ndiponso zinthu zinkapita m'tsogolo mu mzinda wa Yerusalemu ndi m'mizinda yake yozungulira, ku madera a kumwera ndi ku chigwa.’ ” Onani mutuwoMawu a Mulungu mu Chichewa Chalero7 Kodi awa si mawu amene Yehova ankanena kudzera mwa aneneri oyamba aja pamene Yerusalemu ndi mizinda yake yozungulira anali pa mtendere ndi pa ulemerero, ndi pamene Negevi ndi ku madera akumadzulo a mʼmbali mwa phiri munali anthu?’ ” Onani mutuwo |
Anthu adzagula minda ndi ndalama, adzalembera makalata ogulira, adzawasindikiza, adzaitana mboni, m'dziko la Benjamini, ndi m'malo ozungulira Yerusalemu, ndi m'mizinda ya Yuda, ndi m'mizinda ya kumtunda, ndi m'mizinda ya kuchidikha, ndi m'mizinda ya kumwera; pakuti ndidzabweza undende wao, ati Yehova.