Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Zekariya 6:8 - Buku Lopatulika

8 Ndipo anandiitana, nanena nane, kuti, Taonani, iwo akutuluka kunka kudziko la kumpoto anapumulitsa Mzimu wanga m'dziko la kumpoto.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

8 Ndipo anandiitana, nanena nane, kuti, Taonani, iwo akutuluka kunka kudziko la kumpoto anapumulitsa Mzimu wanga m'dziko la kumpoto.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

8 Apo mngeloyo adandiŵuza mokweza mau kuti, “Amene apita ku dziko lakumpotowo atsitsa mzimu wanga kumeneko.”

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

8 Pamenepo anandiyitana, “Taona, akavalo amene apita ku dziko la kumpoto apumulitsa Mzimu wanga kumeneko.”

Onani mutuwo Koperani




Zekariya 6:8
15 Mawu Ofanana  

Ngati mkulu akukwiyira, usasiye malo ako; chifukwa chifatso chipembedza utachimwa kwambiri.


Chifukwa chake Ambuye ati, Yehova wa makamu wamphamvu wa Israele, Ha! Ndidzatonthoza mtima wanga pochotsa ondivuta, ndi kubwezera chilango adani anga;


Sonkhanani inu nonse ndi kumva, ndani mwa iwo aonetsa zinthu izi? Iye amene Yehova anamkonda, iye adzachita kufuna kwake pa Babiloni, ndi mkono wake udzakhala pa Ababiloni.


M'mwemo ukali wanga udzakhuta nawe, ndi nsanje yanga idzakuchokera, ndipo ndidzakhala chete wosakwiyanso.


kuti uzikumbukira ndi kuchita manyazi ndi kusatsegulanso pakamwa pako konse, chifukwa chamanyazi ako, pamene ndikufafanizira zonse unazichita, ati Ambuye Yehova.


M'chodetsa chako muli dama, popeza ndinakuyeretsa; koma sunayeretsedwa, sudzayeretsedwanso kukuchotsera chodetsa chako, mpaka nditakwaniritsa ukali wanga pa iwe.


Motero mkwiyo wanga udzakwaniridwa, ndipo ndidzakhutitsa ukali wanga pa iwo, ndi kudzitonthoza; ndipo adzadziwa kuti Ine Yehova ndinanena m'changu changa, pokwaniridwa nao ukali wanga.


Ndipo ndikwiya nao amitundu okhala osatekeseka ndi mkwiyo waukulu; pakuti ndinakwiya pang'ono, ndipo anathandizira choipa.


Ndipo Samisoni ananena nao, Mukatero ndidzakubwezerani chilango ndi pamenepo ndidzaleka.


Mulungu anapereka m'dzanja lanu akalonga a Midiyani, Orebu ndi Zeebu, ndipo ndinakhoza kuchitanji monga inu? Pamenepo mkwiyo wao unamlezera, atanena mau awa.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa