Zekariya 4:7 - Buku Lopatulika7 Ndiwe yani, phiri lalikulu iwe? Pamaso pa Zerubabele udzasanduka chidikha; ndipo adzatulutsa mwala woikidwa pamwamba, ndi kufuula, Chisomo, chisomo nao. Onani mutuwoChichewa Buku Lopatulika Bible 20147 Ndiwe yani, phiri lalikulu iwe? Pamaso pa Zerubabele udzasanduka chidikha; ndipo adzatulutsa mwala woikidwa pamwamba, ndi kufuula, Chisomo, chisomo nao. Onani mutuwoBuku Loyera Catholic Edition - Chichewa7 Kodi iwe phiri lalitali, ndiwenso chiyani? Udzasanduka dziko losalala pamaso pa Zerubabele. Ndipo akadzabwera nawo mwala wotsiriza wa pa Nyumba yanga, namauika pamwamba, anthu adzafuula kuti, ‘Ati kukongola ati!’ ” Onani mutuwoMawu a Mulungu mu Chichewa Chalero7 “Kodi ndiwe yani, iwe phiri lamphamvu? Pamaso pa Zerubabeli udzasanduka dziko losalala. Pamenepo adzabweretsa mwala wotsiriza. Akamadzawuyika pamwamba anthu adzafuwula kuti, ‘Mulungu adalitse Nyumbayi! Mulungu adalitse Nyumbayi!’ ” Onani mutuwo |
mudzamvekanso mau akukondwa ndi mau akusekera, mau a mkwati ndi mau a mkwatibwi, mau a iwo akuti, Myamikireni Yehova wa makamu, pakuti Yehova ndiye wabwino, chifundo chake nchosatha; ndi a iwo akutengera nsembe zoyamikira m'nyumba ya Yehova. Pakuti ndidzabweza undende wa dziko monga poyamba, ati Yehova.