Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Zekariya 11:8 - Buku Lopatulika

8 Ndipo ndinatha abusa atatuwo mwezi umodzi; pakuti mtima wanga unalema nao, ndi mtima waonso unaipidwa nane.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

8 Ndipo ndinatha abusa atatuwo mwezi umodzi; pakuti mtima wanga unalema nao, ndi mtima waonso unaipidwa nane.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

8 Pa mwezi umodzi ndidachotsa abusa atatu aja. Adafika pondipsetsa mtima, ine osathanso kuŵapirira. Iwonso adadana nane.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

8 Pa mwezi umodzi ndinachotsa abusa atatu. Abusawo anadana nane, ndipo ndinatopa nawo.

Onani mutuwo Koperani




Zekariya 11:8
25 Mawu Ofanana  

Ndipo iye anali mdani wa Israele masiku onse a Solomoni, kuonjezerapo choipa anachichita Hadadi, naipidwa nao Aisraele, nakhala mfumu ya ku Aramu.


Potero udayaka mkwiyo wa Yehova pa anthu ake, nanyansidwa Iye ndi cholowa chake.


Opusa sadzakhazikika pamaso panu, mudana nao onse akuchita zopanda pake.


Ana a Efuremu okhala nazo zida, oponya nao mauta, anabwerera m'mbuyo tsiku la nkhondo.


Atero Yehova, Mombolo wa Israele, ndi Woyera wake, kwa Iye amene anthu amnyoza, kwa Iye amene mtundu wathu unyasidwa naye, kwa mtumiki wa olamulira: Mafumu adzaona, nadzauka; akalonga nadzalambira chifukwa cha Yehova, amene ali wokhulupirika, ngakhale Woyera wa Israele, amene anakusankha Iwe.


Cholowa changa chandisandukira mkango wa m'nkhalango; anatsutsana nane ndi mau ake; chifukwa chake ndinamuda.


Musatinyoze ife, chifukwa cha dzina lanu; musanyazitse mpando wachifumu wa ulemerero wanu; mukumbukire musasiye pangano lanu lopangana ndi ife.


Anthu adzawatcha nthale ya siliva, pakuti Yehova wakana iwo.


kuti ndigwire nyumba ya Israele mumtima mwao; popeza onsewo asanduka alendo ndi Ine mwa mafano ao.


Iwe ndiwe mwana wa mai ako wonyansidwa naye mwamuna wake ndi ana ake, ndipo iwe ndiwe mng'ono wao wa akulu ako akunyansidwa ndi amuna ao ndi ana ao; mai wako ndiye Muhiti, ndi atate wako ndiye Mwamori.


Anthu anga aonongeka chifukwa cha kusadziwa; popeza unakana kudziwa, Inenso ndikukaniza, kuti usakhale wansembe wanga; popeza waiwala chilamulo cha Mulungu wako, Inenso ndidzaiwala ana ako.


Anachita mosakhulupirika pa Yehova, pakuti anabala ana achilendo; mwezi wokhala udzawatha tsopano, pamodzi ndi maiko ao.


Choipa chao chonse chili mu Giligala; pakuti pamenepo ndinawada, chifukwa cha kuipa kwa machitidwe ao ndidzawainga kuwachotsa m'nyumba mwanga; sindidzawakondanso; akalonga ao onse ndiwo opanduka.


Ndidzamanga Kachisi wanga pakati pa inu, ndipo moyo wanga sudzanyansidwa nanu.


Ndipo ndidzaononga malo amsanje anu, ndi kulikha zoimiritsa zanu za dzuwa, ndi kuponya mitembo yanu pa mitembo ya mafano anu; ndi moyo wanga udzanyansidwa nanu.


Ndiponso pali ichinso: pokhala iwo m'dziko la adani ao sindidzawakaniza, kapena kunyansidwa nao, kuwaononga konse, ndi kuthyola pangano langa ndinapangana nao; popeza Ine ndine Yehova Mulungu wao.


Koma ndili ndi ubatizo ndikabatizidwe nao; ndipo ndikanikizidwa Ine kufikira ukatsirizidwa!


Koma mfulu za pamudzi pake zinamuda, nkutuma akazembe amtsate m'mbuyo ndi kunena, Ife sitifuna munthuyo akhale mfumu yathu.


Ngati dziko lapansi lida inu, mudziwa kuti lidada Ine lisanayambe kuda inu.


Dziko lapansi silingathe kudana ndi inu; koma Ine lindida popeza Ine ndilichitira umboni, kuti ntchito zake zili zoipa.


Ndipo Yehova anachiona, nawanyoza, pakuipidwa nao ana ake aamuna, ndi akazi.


Koma wolungama wangayo adzakhala ndi moyo wochokera m'chikhulupiriro: Ndipo ngati abwerera, moyo wanga ulibe kukondwera mwa iye.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa