Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Zekariya 11:5 - Buku Lopatulika

5 zimene eni ake azipha, nadziyesera osapalamula; ndi iwo akuwagulitsa akuti, Alemekezedwe Yehova, pakuti ine ndine wolemera; ndi abusa ao sazichitira chifundo.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

5 zimene eni ake azipha, nadziyesera osapalamula; ndi iwo akuwagulitsa akuti, Alemekezedwe Yehova, pakuti ine ndine wolemera; ndi abusa ao sazichitira chifundo.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

5 Amene amagula nkhosa amazipha, koma salangidwa. Amene amazigulitsa amanena kuti, ‘Atamandike Chauta, ine ndalemera!’ Ndipo abusa ake sadzazimvera chifundo nkhosazo.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

5 Amene amagula nkhosazo amazipha ndipo salangidwa. Amene amazigulitsa amanena kuti, ‘Alemekezeke Yehova, ine ndalemera!’ Abusa ake omwe sazimvera chisoni nkhosazo.

Onani mutuwo Koperani




Zekariya 11:5
27 Mawu Ofanana  

Ndipo wina wa akazi a ana a aneneri anafuula kwa Elisa, ndi kuti, Mnyamata wanu, mwamuna wanga wafa; mudziwa kuti mnyamata wanu anaopa Yehova; ndipo wafika wamangawa kunditengera ana anga awiri akhale akapolo ake.


Ndipo ndinanena nao, Ife monga umo tinakhoza, tinaombola abale athu Ayuda ogulitsidwa kwa amitundu; ndipo kodi inu mukuti mugulitse abale anu, kapena tiwagule ndi ife? Pamenepo anakhala duu, nasowa ponena.


Israele anali wopatulikira Yehova, zipatso zoyamba za zopindula zake; onse amene adzamudya iye adzayesedwa opalamula; choipa chidzawagwera, ati Yehova.


Onse amene anazipeza anazidya; adani ao anati, Sitipalamula mlandu, chifukwa iwo anachimwira Yehova, ndiye mokhalamo zolungama, Yehova, chiyembekezo cha atate ao.


Atero Ambuye Yehova, Taonani, Ine ndiipidwa nao abusa, ndidzafunsa nkhosa zanga padzanja lao, ndi kuwaletsa asadyetsenso nkhosazo, ngakhale kudzidyetsa okha sadzachitanso; ndipo ndidzalanditsa nkhosa zanga pakamwa pao, zisakhale chakudya chao.


Popeza mukankha ndi nthiti ndi phewa, nimugunda zodwala zonse ndi nyanga zanu, mpaka mwazibalalitsa kubwalo,


Nkhosa zanga zinasokera kumapiri ali onse, ndi pa chitunda chilichonse chachitali; inde nkhosa zanga zinabalalika padziko lonse lapansi, ndipo panalibe wakuzipwaira kapena kuzifunafuna.


Ndipo Efuremu anati, Zedi ndasanduka wolemera, ndadzionera chuma m'ntchito zonse ndinazigwira; sadzapeza mwa ine mphulupulu yokhala tchimo.


Koma Ine ndine Yehova Mulungu wako chichokere dziko la Ejipito, ndidzakukhalitsanso m'mahema, monga masiku a zikondwerero zoikika.


Atero Yehova, Chifukwa cha zolakwa zitatu za Israele, kapena zinai, sindidzabweza kulanga kwake; popeza agulitsa wolungama ndi ndalama, ndi wosowa chifukwa cha nsapato;


Koma tsoka inu, alembi ndi Afarisi, onyenga! Chifukwa mutsekera anthu Ufumu wa Kumwamba pamaso pao; pakuti inu nokha simulowamo, ndipo muwaletsa amene alikulowa, kuti asalowemo.


Indetu, indetu, ndinena ndi inu, Iye wosalowa m'khola la nkhosa pakhomo, koma akwerera kwina, iyeyu ndiye wakuba ndi wolanda.


Adzakutulutsani m'masunagoge, koma ikudza nthawi imene yense wakupha inu adzayesa kuti atumikira Mulungu.


Ndipo m'chisiriro adzakuyesani malonda ndi mau onyenga; amene chiweruzo chao sichinachedwe ndi kale lomwe, ndipo chitayiko chao sichiodzera.


ndi sinamoni ndi amomo, ndi zofukiza, ndi mure, ndi lubani, ndi vinyo, ndi mafuta, ndi ufa wosalala, ndi tirigu, ndi ng'ombe, ndi nkhosa; ndi malonda a akavalo, ndi a magaleta, ndi a anthu ndi a miyoyo ya anthu.


Chifukwa unena kuti ine ndine wolemera, ndipo chuma ndili nacho, osasowa kanthu; ndipo sudziwa kuti ndiwe watsoka, ndi wochititsa chifundo, ndi wosauka, ndi wakhungu, ndi wausiwa;


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa