Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Yoswa 7:3 - Buku Lopatulika

3 Ndipo anabwera kwa Yoswa, nati kwa iye, Asakwere anthu onse; koma akwere amuna ngati zikwi ziwiri kapena zitatu kukantha Ai; musalemetsa anthu onse kunkako, pakuti a komweko ndi owerengeka.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

3 Ndipo anabwera kwa Yoswa, nati kwa iye, Asakwere anthu onse; koma akwere amuna ngati zikwi ziwiri kapena zitatu kukantha Ai; musalemetsa anthu onse kumkako, pakuti a komweko ndi owerengeka.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

3 Atabwerera kwa Yoswa, anthuwo adamuuza kuti, “Sikofunikira kuti tipite tonse kumeneko. Ingotumani anthu zikwi ziŵiri kapena zitatu kuti akathire nkhondo mzinda wa Ai. Musatume anthu onse kumeneko poti si mzinda waukulu.”

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

3 Atabwera kwa Yoswa, anamuwuza kuti, “Sikofunika kuti apite anthu onse kukathira nkhondo mzinda wa Ai. Mutumizeko anthu 2,000 kapena 3,000 kuti akatenge mzindawo. Musawatume anthu onse kumeneko popeza kuli anthu ochepa.”

Onani mutuwo Koperani




Yoswa 7:3
9 Mawu Ofanana  

Moyo wa waulesi ukhumba osalandira kanthu; koma moyo wa akhama udzalemera.


Chifuniro cha waulesi chimupha; chifukwa manja ake akana kugwira ntchito.


Yesetsani kulowa pa khomo lopapatiza; chifukwa anthu ambiri, ndikuuzani, adzafunafuna kulowamo, koma sadzakhoza.


Chifukwa chake tichite changu cha kulowa mpumulowo, kuti wina angagwe m'chitsanzo chomwe cha kusamvera.


Ndipo Yoswa anatuma amuna kuchokera ku Yeriko apite ku Ai, ndiwo pafupi pa Betaveni, kum'mawa kwa Betele; nanena nao, Kwerani ndi kukazonda dziko. Nakwera amunawo, nazonda Ai.


Potero mwa anthu anakwerako amuna monga zikwi zitatu; koma anathawa pamaso pa amuna a ku Ai.


Momwemo abale, onjezani kuchita changu kukhazikitsa maitanidwe ndi masankhulidwe anu; pakuti mukachita izi, simudzakhumudwa nthawi zonse;


Ndipo mwa ichi chomwe, pakutengeraponso changu chonse, muonjezerapo ukoma pa chikhulupiriro chanu, ndi paukoma chizindikiritso;


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa