Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Yohane 9:32 - Buku Lopatulika

32 Kuyambira pachiyambi sikunamveke kuti wina anatsegulira maso munthu wosaona chibadwire.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

32 Kuyambira pachiyambi sikunamveka kuti wina anatsegulira maso munthu wosaona chibadwire.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

32 Nkale lomwe sikudamveke konse kuti wina adapenyetsa munthu wakhungu.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

32 Palibe amene anamvapo za kutsekula maso a munthu wobadwa wosaona.

Onani mutuwo Koperani




Yohane 9:32
7 Mawu Ofanana  

Kodi suchidziwa ichi chiyambire kale lomwe, kuyambira anaika munthu padziko lapansi,


Pakuti kuyambira kale anthu sanamve pena kumvetsa ndi khutu, ngakhale diso silinaone Mulungu wina popanda Inu, amene amgwirira ntchito iye amene amlindirira Iye.


Monga Iye analankhula ndi m'kamwa mwa aneneri ake oyera mtima, akale lomwe,


Ena ananena, Mau awa sali a munthu wogwidwa chiwanda. Kodi chiwanda chikhoza kumtsegulira maso wosaona?


Tidziwa kuti Mulungu samvera ochimwa. Koma ngati munthu aliyense akhala wopembedza Mulungu nachita chifuniro chake, amvera ameneyo.


Ngati uyu sanachokere kwa Mulungu, sakadakhoza kuchita kanthu.


ndipo panakhala mphezi, ndi mau, ndi mabingu; ndipo panali chivomezi chachikulu chotero sichinaoneke chiyambire anthu padziko, chivomezi cholimba chotero, chachikulu chotero.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa