Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Yohane 9:22 - Buku Lopatulika

22 Izi ananena atate wake ndi amake, chifukwa anaopa Ayuda; pakuti Ayuda adapangana kale, kuti ngati munthu aliyense adzamvomereza Iye kuti ndiye Khristu, akhale woletsedwa m'sunagoge.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

22 Izi ananena atate wake ndi amake, chifukwa anaopa Ayuda; pakuti Ayuda adapangana kale, kuti ngati munthu aliyense adzamvomereza Iye kuti ndiye Khristu, akhale woletsedwa m'sunagoge.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

22 Makolo akewo adaatero chifukwa ankaopa akulu a Ayuda. Pakuti Ayuda anali atapangana kale kuti, ngati munthu adzavomereza kuti Yesu ndiye Mpulumutsi wolonjezedwa uja, adzamdula ku mpingo.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

22 Makolo ake ananena izi chifukwa amaopa Ayuda, popeza Ayuda anatsimikiza kale kuti aliyense amene adzamuvomereza Yesu kuti anali Khristu adzatulutsidwa mʼsunagoge.

Onani mutuwo Koperani




Yohane 9:22
24 Mawu Ofanana  

Kuopa anthu kutchera msampha; koma wokhulupirira Yehova adzapulumuka.


Ine, Inedi, ndine amene nditonthoza mtima wako; kodi iwe ndani, kuti uopa munthu amene adzafa, ndi mwana wa munthu amene adzakhala ngati udzu;


Mverani Ine, inu amene mudziwa chilungamo, anthu amene mumtima mwao muli lamulo langa; musaope chitonzo cha anthu, ngakhale kuopsedwa ndi kutukwana kwao.


Ndipo ndi yani amene wamuopa ndi kuchita naye mantha, kuti wanama, osandikumbukira Ine, kapena kundisamalira? Kodi Ine sindinakhale chete nthawi yambiri, ndipo iwe sunandiope Ine konse?


Odala inu, pamene anthu adzada inu, nadzapatula inu, nadzatonza inu, nadzalitaya dzina lanu monga loipa, chifukwa cha Mwana wa Munthu.


Ndipo umene ndiwo umboni wa Yohane, pamene Ayuda anatuma kwa iye ansembe ndi Alevi a ku Yerusalemu akamfunse iye, Ndiwe yani?


Adzakutulutsani m'masunagoge, koma ikudza nthawi imene yense wakupha inu adzayesa kuti atumikira Mulungu.


Chitatha ichi Yosefe wa ku Arimatea, ndiye wophunzira wa Yesu, koma mobisika, chifukwa cha kuopa Ayuda, anapempha Pilato kuti akachotse mtembo wa Yesu. Ndipo Pilato analola. Chifukwa chake anadza, nachotsa mtembo wake.


Pamenepo, pokhala madzulo, tsiku lomwelo, loyamba la Sabata, makomo ali chitsekere, kumene anakhala ophunzira, chifukwa cha kuopa Ayuda, Yesu anadza naimirira pakati pao, nanena nao, Mtendere ukhale ndi inu.


Chinkana anatero panalibe munthu analankhula za Iye poyera, chifukwa cha kuopa Ayuda.


Chifukwa chake Ayuda sanakhulupirire za iye, kuti anali wosaona, napenya, kufikira kumene adaitana atate wake ndi amake a iye wopenya;


koma sitidziwa uno apenyera tsopano; kapena sitimdziwa mene anamtsegulira pamaso pake; mumfunse iye; ali wamsinkhu; adzalankhula mwini za iye yekha.


Anayankha nati kwa iye, Wabadwa iwe konse m'zoipa, ndipo iwe utiphunzitse ife kodi? Ndipo anamtaya kunja.


Yesu anamva kuti adamtaya kunja; ndipo pakumpeza iye, anati, Kodi ukhulupirira Mwana wa Munthu?


Ndipo anawaitana, nawalamulira kuti asanene konse kapena kuphunzitsa m'dzina la Yesu.


Koma palibe mmodzi wa otsalawo analimba mtima kuphatikana nao; komatu anthu anawakuzitsa;


Ndipo anavomerezana ndi iye; ndipo m'mene adaitana atumwi, anawakwapula nawalamulira asalankhule kutchula dzina la Yesu, ndipo anawamasula.


Koma amantha, ndi osakhulupirira, ndi onyansa, ndi ambanda, ndi achigololo, ndi olambira mafano, ndi onse a mabodza, cholandira chao chidzakhala m'nyanja yotentha ndi moto ndi sulufure; ndiyo imfa yachiwiri.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa