Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Yohane 8:42 - Buku Lopatulika

42 Yesu anati kwa iwo, Mulungu akadakhala Atate wanu, mukadakonda Ine; pakuti Ine ndinatuluka, ndi kuchokera kwa Mulungu; pakuti sindinadze kwa Ine ndekha, koma Iyeyu anandituma Ine.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

42 Yesu anati kwa iwo, Mulungu akadakhala Atate wanu, mukadakonda Ine; pakuti Ine ndinatuluka, ndi kuchokera kwa Mulungu; pakuti sindinadza kwa Ine ndekha, koma Iyeyu anandituma Ine.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

42 Yesu adati, “Mulungu akadakhaladi Atate anu, bwenzi mutandikonda Ine, chifukwa ndidafumira kwa Mulungu, ndipo tsopano ndili kuno. Sindidabwere ndi ulamuliro wa Ine ndekha ai, koma Iyeyo adachita kundituma.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

42 Yesu anawawuza kuti, “Mulungu akanakhala Atate anu, inu mukanandikonda Ine, pakuti Ine ndinachokera kwa Mulungu ndipo tsopano ndili pano. Ine sindinabwere mwa Ine ndekha.

Onani mutuwo Koperani




Yohane 8:42
22 Mawu Ofanana  

Mwana alemekeza atate wake, ndi mnyamata mbuye wake; ngati Ine tsono ndine atate, uli kuti ulemu wanga? Ngati Ine ndine mbuye, kundiopa kuli kuti? Ati Yehova wa makamu kwa inu ansembe akupeputsa dzina langa. Ndipo mukuti, Tapeputsa dzina lanu motani?


Ndipo Mau anasandulika thupi, nakhazikika pakati pa ife, ndipo tinaona ulemerero wake, ulemerero wonga wa wobadwa yekha wa Atate, wodzala ndi chisomo ndi choonadi.


Pakuti sindinalankhule mwa Ine ndekha; koma Atate wondituma Ine, yemweyu anandipatsa Ine lamulo, limene ndikanene, ndi limene ndikalankhule.


Yesu, podziwa kuti Atate adampatsa Iye zonse m'manja mwake, ndi kuti anachokera kwa Mulungu, namuka kwa Mulungu,


Sukhulupirira kodi kuti ndili Ine mwa Atate, ndi Atate ali mwa Ine? Mau amene ndinena Ine kwa inu sindilankhula kwa Ine ndekha; koma Atate wokhala mwa Ine achita ntchito zake.


Tsopano tidziwa kuti mudziwa zonse, ndipo mulibe kusowa kuti wina akafunse Inu; mwa ichi tikhulupirira kuti munatuluka kwa Mulungu.


Atate wolungama, dziko lapansi silinadziwe Inu, koma Ine ndinadziwa Inu; ndipo iwo anazindikira kuti munandituma Ine;


chifukwa mau amene munandipatsa Ine ndinapatsa iwo; ndipo analandira, nazindikira koona kuti ndinatuluka kwa Inu, ndipo anakhulupirira kuti Inu munandituma Ine.


Pakuti Mulungu sanatume Mwana wake kudziko lapansi, kuti akaweruze dziko lapansi, koma kuti dziko lapansi likapulumutsidwe ndi Iye.


kuti onse akalemekeze Mwana, monga alemekeza Atate. Wosalemekeza Mwana salemekeza Atate amene anamtuma Iye.


Ndadza Ine m'dzina la Atate wanga, ndipo simundilandira Ine; akadza wina m'dzina lake la iye mwini, iyeyu mudzamlandira.


Anayankha Yesu nati kwa iwo, Ndingakhale ndichita umboni wa Ine ndekha umboni wanga uli woona; chifukwa ndidziwa kumene ndinachokera ndi kumene ndimukako; koma inu simudziwa kumene ndichokera, ndi kumene ndimukako.


Ngati wina sakonda Ambuye, akhale wotembereredwa. Akudza Ambuye.


koma pokwaniridwa nthawi, Mulungu anatuma Mwana wake, wobadwa ndi mkazi, wobadwa wakumvera lamulo,


Ndipo ife tapenyera, ndipo tichita umboni kuti Atate anatuma Mwana akhale Mpulumutsi wa dziko lapansi.


Ndipo tidziwa kuti Mwana wa Mulungu wafika, natipatsa ife chidziwitso, kuti tizindikire Woonayo, ndipo tili mwa Woonayo, mwa Mwana wake Yesu Khristu. Iye ndiye Mulungu woona ndi moyo wosatha.


Ndipo anandionetsa mtsinje wa madzi a moyo, wonyezimira ngati krustalo, otuluka kumpando wachifumu wa Mulungu ndi wa Mwanawankhosa.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa