Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Yohane 8:39 - Buku Lopatulika

39 Anayankha nati kwa iye, Atate wathu ndiye Abrahamu. Yesu ananena nao, Ngati muli ana a Abrahamu, mukadachita ntchito za Abrahamu.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

39 Anayankha nati kwa iye, Atate wathu ndiye Abrahamu. Yesu ananena nao, Ngati muli ana a Abrahamu, mukadachita ntchito za Abrahamu.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

39 Iwo adati, “Ifetu atate athu ndi Abrahamu.” Yesu adaŵauza kuti, “Mukadakhala ana a Abrahamu, bwenzi mukuchita zimene Abrahamuyo ankachita.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

39 Iwo anayankha kuti, “Ife abambo athu ndi Abrahamu.” Yesu anati, “Inu mukanakhala ana a Abrahamu, bwenzi mukuchita zinthu zimene Abrahamuyo ankachita.

Onani mutuwo Koperani




Yohane 8:39
13 Mawu Ofanana  

ndipo musamayesa kunena mwa inu nokha, Atate wathu tili naye Abrahamu; pakuti ndinena kwa inu kuti mwa miyala iyi Mulungu akhoza kuukitsira Abrahamu ana.


kotero kuti mukakhale ana a Atate wanu wa Kumwamba; chifukwa Iye amakwezera dzuwa lake pa oipa ndi pa abwino, namavumbitsira mvula pa olungama ndi pa osalungama.


Anamyankha iye, Tili mbeu ya Abrahamu, ndipo sitinakhale akapolo a munthu nthawi iliyonse; munena bwanji, Mudzayesedwa afulu?


Ndidziwa kuti muli mbeu ya Abrahamu; koma mufuna kundipha Ine, chifukwa mau anga alibe malo mwa inu.


Simuzindikira malankhulidwe anga chifukwa ninji? Chifukwa simungathe kumva mau anga.


Atate wanu Abrahamu anakondwera kuona tsiku langa; ndipo anaona nasangalala.


ndiponso kholo la mdulidwe wa iwo amene siali a mdulidwe okha, koma wa iwo amene atsata mayendedwe a chikhulupiriro chija cha kholo lathu Abrahamu, chimene iye anali nacho asanadulidwe.


Chifukwa chake chilungamo chichokera m'chikhulupiriro, kuti chikhale monga mwa chisomo; kuti lonjezo likhale lokhazikika kwa mbeu zonse; si kwa iwo a chilamulo okhaokha, koma kwa iwonso a chikhulupiriro cha Abrahamu; ndiye kholo la ife tonse;


kapena chifukwa ali mbeu ya Abrahamu, siali onse ana; koma anati, Mwa Isaki, mbeu yako idzaitanidwa.


Koma ngati muli a Khristu, muli mbeu ya Abrahamu, nyumba monga mwa lonjezano.


chotero zindikirani kuti iwo a chikhulupiriro ndiwo ana a Abrahamu.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa