Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Yohane 7:26 - Buku Lopatulika

26 Ndipo taona amalankhula poyera, ndipo sanena kanthu kwa Iye. Kapena kodi akulu adziwa ndithu kuti ndiye Khristu ameneyo?

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

26 Ndipo taona amalankhula poyera, ndipo sanena kanthu kwa Iye. Kapena kodi akulu adziwa ndithu kuti ndiye Khristu ameneyo?

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

26 Si uyu akulankhula poyerayu, popandanso wonenapo kanthu! Kodi kapenatu ndiye kuti akuluakulu akuzindikiradi kuti ameneyu ndiye Mpulumutsi wolonjezedwa uja eti?

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

26 Uyu ali apa, kuyankhula poyera, ndipo iwo sakunena kanthu kwa Iye. Kodi olamulira atsimikizadi kuti Iye ndi Khristu?

Onani mutuwo Koperani




Yohane 7:26
21 Mawu Ofanana  

Woipa athawa palibe momthamangitsa; koma olungama alimba mtima ngati mkango.


Iye sadzalephera kapena kudololoka, kufikira atakhazikitsa chiweruzo m'dziko lapansi; ndipo zisumbu zidzalindira chilamulo chake.


Ndipo anatumiza kwa Iye ophunzira ao, pamodzi ndi Aherode, amene ananena, Mphunzitsi, tidziwa kuti muli woona, ndipo muphunzitsa njira ya Mulungu moona ndithu, ndipo simusamala munthu aliyense; pakuti simuyang'anira pa nkhope ya anthu.


Ndipo Pilato anaitana ansembe aakulu, ndi akulu, ndi anthu, asonkhane,


Koma Afarisi ndi achilamulo anakaniza uphungu wa Mulungu kwa iwo okha, popeza sanabatizidwe ndi iye.


Kungakhale kotero, ambiri a mwa akulu anakhulupirira Iye; koma chifukwa cha Afarisi sanavomereze, kuti angaletsedwe m'sunagoge,


Yesu anayankha iye, Ine ndalankhula zomveka kwa dziko lapansi; ndinaphunzitsa Ine nthawi zonse m'sunagoge ndi mu Kachisi, kumene amasonkhana Ayuda onse; ndipo mobisika sindinalankhule kanthu.


Koma panali munthu wa Afarisi, dzina lake Nikodemo, mkulu wa Ayuda.


Tiyeni, mukaone munthu, amene anandiuza zinthu zilizonse ndinazichita: ameneyu sali Khristu nanga?


Pamenepo ena a iwo a ku Yerusalemu ananena, Kodi suyu amene afuna kumupha?


Koma ambiri a m'khamu la anthu anakhulupirira Iye; ndipo ananena, Pamene Khristu akadza kodi adzachita zizindikiro zambiri zoposa zimene adazichita ameneyo?


Kodi wina wa akulu anakhulupirira Iye, kapena wa Afarisi?


Izi ananena atate wake ndi amake, chifukwa anaopa Ayuda; pakuti Ayuda adapangana kale, kuti ngati munthu aliyense adzamvomereza Iye kuti ndiye Khristu, akhale woletsedwa m'sunagoge.


Koma pakuona kulimbika mtima kwa Petro ndi Yohane, ndipo pozindikira kuti ndiwo anthu osaphunzira ndi opulukira, anazizwa ndipo anawazindikira, kuti adakhala pamodzi ndi Yesu.


ndi kuti unyinji wa abale mwa Ambuye, pokhulupirira m'zomangira zanga, alimbika mtima koposa kulankhula mau a Mulungu opanda mantha.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa