Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Yohane 4:48 - Buku Lopatulika

48 Pamenepo Yesu anati kwa iye, Ngati simuona zizindikiro ndi zozizwa, simudzakhulupirira.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

48 Pamenepo Yesu anati kwa iye, Ngati simuona zizindikiro ndi zozizwa, simudzakhulupirira.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

48 Yesu adamuuza kuti, “Mukapanda kuwona zizindikiro ndi zozizwitsa, simukhulupirira ai.”

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

48 Yesu anawawuza iwo kuti, “Anthu inu pokhapokha mutaona zizindikiro zodabwitsa, simudzakhulupirira.”

Onani mutuwo Koperani




Yohane 4:48
29 Mawu Ofanana  

Chandikomera kuonetsa zizindikiro ndi zozizwa, zimene anandichitira Mulungu Wam'mwambamwamba.


Iye apulumutsa, nalanditsa, nachita zizindikiro ndi zozizwa m'mwamba ndi padziko lapansi, ndiye amene anapulumutsa Daniele kumphamvu ya mikango.


Ndipo Yehova anati kwa Mose, Anthu awa adzaleka liti kundinyoza? Ndipo adzayamba liti kundikhulupirira, chinkana zizindikiro zonse ndinazichita pakati pao?


Ndipo Afarisi ndi Asaduki anadza, namuyesa, namfunsa Iye awaonetse chizindikiro cha Kumwamba.


chifukwa Akhristu onama adzauka, ndi aneneri onama nadzaonetsa zizindikiro zazikulu ndi zozizwa: kotero kuti akanyenge, ngati nkotheka, osankhidwa omwe. Onani ndakuuziranitu pasadafike.


Anapulumutsa ena, sangathe kudzipulumutsa yekha. Ndiye mfumu ya Aisraele; atsike tsopano pamtandapo, ndipo tidzamkhulupirira Iye.


pakuti adzauka Akhristu onyenga ndi aneneri onyenga, ndipo adzachita zizindikiro ndi zozizwitsa, kuti akasocheretse, ngati nkutheka, osankhidwa omwe.


Ndipo anati kwa iwo, Ndinaona Satana alinkugwa ngati mphezi wochokera kumwamba.


Koma anati kwa iye, Ngati samvera Mose ndi aneneri, sadzakopeka mtima ngakhale wina akauka kwa akufa.


Koma angakhale adachita zizindikiro zambiri zotere pamaso pao iwo sanakhulupirire Iye;


Sindikadachita mwa iwo ntchito zosachita wina, sakadakhala nalo tchimo; koma tsopano anaona, nada Ine ndi Atate wanganso.


Chifukwa chake Ayuda anayankha nati kwa Iye, Mutionetsera ife chizindikiro chanji, pakuti muchita izi?


Yesu ananena kwa iye, Chifukwa wandiona Ine, wakhulupirira; odala iwo akukhulupirira, angakhale sanaone.


Mkuluyo ananena kwa Iye, Ambuye, tsikani asanafe mwana wanga.


Chifukwa chake anakhala nthawi yaikulu nanenetsa zolimba mtima mwa Ambuye, amene anachitira umboni mau a chisomo chake, napatsa zizindikiro ndi zozizwa kuti zichitidwe ndi manja ao.


Ndipo khamu lonse linatonthola; ndipo anamvera Barnabasi ndi Paulo alikubwerezanso zizindikiro ndi zozizwitsa zimene Mulungu anachita nao pa amitundu.


Ndipo ndidzapatsa zodabwitsa m'thambo la kumwamba, ndi zizindikiro padziko lapansi; mwazi, ndi moto, ndi mpweya wa utsi;


Amuna inu Aisraele, mverani mau awa: Yesu Mnazarayo, mwamuna wochokera kwa Mulungu, wosonyezedwa kwa inu ndi zimphamvu, ndi zozizwa, ndi zizindikiro, zimene Mulungu anazichita mwa Iye pakati pa inu monga mudziwa nokha;


Koma panadza mantha pa anthu onse; ndipo zozizwa ndi zizindikiro zambiri zinachitika ndi atumwi.


m'mene mutambasula dzanja lanu kukachiritsa; ndi kuti zizindikiro ndi zozizwa zichitidwe mwa dzina la Mwana wanu wopatulika Yesu.


Ndipo mwa manja a atumwi zizindikiro ndi zozizwa zambiri zinachitidwa pa anthu; ndipo anali onse ndi mtima umodzi m'khonde la Solomoni.


Ndipo Stefano, wodzala ndi chisomo ndi mphamvu, anachita zozizwa ndi zizindikiro zazikulu mwa anthu.


Ameneyo anawatsogolera, natuluka nao atachita zozizwa ndi zizindikiro mu Ejipito, ndi mu Nyanja Yofiira, ndi m'chipululu zaka makumi anai.


mu mphamvu ya zizindikiro ndi zozizwitsa, mu mphamvu ya Mzimu Woyera; kotero kuti ine kuyambira ku Yerusalemu ndi kuzungulirako kufikira ku Iliriko, ndinakwanitsa Uthenga Wabwino wa Khristu;


Ndipo popeza Ayuda afunsa zizindikiro, ndi Agriki atsata nzeru:


Zizindikirotu za mtumwi zinachitika pakati pa inu, m'chipiriro chonse, ndi zizindikiro, ndi zozizwa, ndi zamphamvu.


ndiye amene kudza kwake kuli monga mwa machitidwe a Satana, mu mphamvu yonse, ndi zizindikiro ndi zozizwa zonama;


pochita umboni pamodzi nao Mulungunso ndi zizindikiro, ndi zozizwitsa ndi mphamvu za mitundumitundu ndi zogawira za Mzimu Woyera, monga mwa chifuniro chake.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa