Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Yohane 4:39 - Buku Lopatulika

39 Ndipo m'mzinda muja anthu Asamariya ambiri anamkhulupirira Iye chifukwa cha mau a mkazi, wochita umboniyo, kuti, Anandiuza ine zinthu zilizonse ndinazichita.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

39 Ndipo m'mudzi muja anthu Asamariya ambiri anamkhulupirira Iye chifukwa cha mau a mkazi, wochita umboniyo, kuti, Anandiuza ine zinthu zilizonse ndinazichita.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

39 Asamariya ambiri a m'mudzi muja adakhulupirira Yesu chifukwa cha umboni wa mai uja, wakuti, “Iye wandiwuza zonse zimene ndidachita.”

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

39 Asamariya ambiri ochokera mʼmudziwo anakhulupirira Iye chifukwa cha umboni wa mayiyo wakuti, “Iye anandiwuza ine zonse ndinazichita.”

Onani mutuwo Koperani




Yohane 4:39
11 Mawu Ofanana  

Awa amene, khumi ndi awiriwa, Yesu anawatumiza, nawalangiza ndi kuti, Musapite kunjira ya kwa anthu akunja, ndi m'mudzi wa Asamariya musamalowamo:


Ndipo ophunzira awiriwo anamva iye alinkulankhula, natsata Yesu.


Chifukwa chake ambiri a mwa Ayuda amene anadza kwa Maria, m'mene anaona chimene anachita, anakhulupirira Iye.


Tiyeni, mukaone munthu, amene anandiuza zinthu zilizonse ndinazichita: ameneyu sali Khristu nanga?


Anatuluka iwo m'mzinda ndipo analinkudza kwa Iye.


Ine ndinatuma inu kukamweta chimene simunagwirirapo ntchito: ena anagwira ntchito, ndipo inu mwalowa ntchito yao.


Chifukwa chake pamene Asamariya anadza kwa Iye, anamfunsa akhale nao; ndipo anakhala komweko masiku awiri.


ndipo ananena kwa mkazi, kuti, Tsopano sitikhulupirira chifukwa cha kulankhula kwako: pakuti tamva tokha, ndipo tidziwa kuti Mpulumutsi wa dziko lapansi ndi Iyeyu ndithu.


Chifukwa chake anadza kumzinda wa Samariya, dzina lake Sikari, pafupi pa kadziko kamene Yakobo adapatsa mwana wake Yosefe;


Pakuti ophunzira ake adachoka kunka kumzinda kuti akagule chakudya.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa